Malawi yaphwasamula Fiji

Advertisement

Timu ya mpira wa manja ya Malawi yasambwadza timu ya dziko la Fiji ndi zigoli 62 kwa 48 mu mpikisano wa dziko lonse la pansi wa Vitality Netball World Cup ku South Africa.

Awa anali masewera oyamba mu ndime yachiwiri ya mpikisanowu ndipo anachitikira pa bwalo la Cape Town International Convention Centre lero.

Malawi yomwe imadziwika ndi dzina loti Queens inayamba bwino mu kota yoyamba pomwe Joyce Mvula ndi Mwai Kumwenda anayaka moto.

Malawi inawina kota yoyamba ndi zigoli 20 kwa 10. Pamene matimuwa amamaliza chigawo choyamba cha masewerowa, Malawi inali ikutsogola ndi zigoli 36 kwa 23.

Mu kota yachitatu matimuwa anafanana mphamvu pomwe timu iliyonse inagoletsa zigoli 11 komabe Malawi inali ikutsogolabe ndi zigoli 47 kwa 34.

Mu kota yomaliza, Malawi inakakamilabe mpaka inawina ndi zigoli 62 kwa 48.

Mawa Malawi isewera ndi timu ya Australia ndipo lachinayi izamenya ndi timu ya Tonga mu ndime yachiwiri yomweyi.

Advertisement