Kwavuta ku Mwanza: anthu akugonana kwambiri, sakudziteteza

Advertisement
MWANZA-DISTRICT-HOSPITAL

Pamene boma komaso mabungwe osiyanasiyana akulimbikitsa kuti anthu azigwiritsa ntchito njira zozitetezera pogonana, zadziwika kuti m’boma la Mwanza sizili choncho, chiwerengero cha odwala matenda opatsirana poganana chakwera kwambiri.

Izi ndimalingana ndi a Samuel Simbi amene ndi m’modzi mwa madotolo akuluakulu pa chipatala cha Mwanza omwe amayankhula ndi imodzi mwa nyumba zofalitsira mawu m’dziko muno.

A Simbi anauza nyumba yowulutsira mawuyo kuti mwezi uno pamene siunathe, m’bomali mwapezeka kale anthu odwala matenda opatsirana pogonana okwana 250, chiwerengero chomwe ndichokwera kwambiri.

Iwo ati kuyambira January kufika mwezi wa May chaka chino, anthu okwana 5,080 anapezeka ndi matenda opatsirana pogonana ndipo ambiri mwa iwo analandira thandizo la mankhwala komaso uphungu.

Izi zikudza kaamba koti boma la Mwanza limadziwika kwambiri ndi ntchito za mtengatenga ndi mtokoma kaamba ka chipata cholowera ndikutulukira m’dziko muno (Mwanza border).

Kaamba ka chipata cha Mwanza, azimayi ochuluka ogulitsa thupi, amakhala mbwelekete zomwe zimapeleka chiopsezo kwa anthu osawugwira mtima makamaka azibambo oyendetsa magalimoto akuluakulu.

Pakadali pano, bungwe la International Organization for Migration (IOM) lakonza ndikupeleka zipangizo zomwe zigwile ntchito pa chipatala chaching’ono pa chipata m’bomali.

A Nomagugu Hanyana Ncube omwe ndi nkulu wa bungwe IOM kuno ku Malawi, ati izi zithandizira anthu oyendetsa galimoto pakati pa dziko lino ndi mayiko ena komanso azimayi ogulitsa matupi kulandira thandizo la mankhwala komanso uphungu wa nkhani zogonanana mwaulele.

Follow us on Twitter:

Advertisement