Ngati munalandira katemera wa AstraZeneca, musabaitsenso wa J&J

Advertisement

Pamene unduna wa zaumoyo ukuyembekeza kulandira katemera wa Johnson and Johnson, undunawu wachenjeza anthu mdziko kuti asalandile katemera wa Johnson and Johnson ngati analandirapo kale wa AstraZeneca.

Mlembi Wamkulu mu Unduna wa Zaumoyo a Dr. Charles Mwansambo ndi omwe anena izi mu chikalata chomwe anatulutsa lachitatu.

Katemera wa mtundu wa Johnson and Johnson yemwe waperekedwa ndi dziko la America wokwana kupereka kwa anthu 302,400 afika m’dziko muno loweruka pa 7th August, 2021.

Katemerayu akuyembekezeka kuyamba kuperekedwa kwa anthu mdziko muno sabata la mawa koma unduna wa zaumoyo wati aliyense yemwe analandirapo katemera wa AstraZeneca, kamodzi kapena kawiri, sakuyenera kubaitsaso.

“Oyenera kulandira katemerayu ndi aliyense amene anakwanitsa zaka 18 kapena kuposera apo. Katemera wa Johnson and Johnson adzaperekedwa kwa okhawo amene sanalandirepo katemera wina aliyense wa COVID-19. Izi zikutanthauza kuti kwa amene analandira katemera woyamba wa mtundu wa AstraZeneca sakuyenera kulandira nawo katemera wa Johnson and Johnson,” anatero a Mwansambo.

Malingana ndi a Mwansambo, amene analandira katemera woyamba wa mtundu wa AstraZeneca akuyenera kudikira kuti adzalandirenso katemera wachiwiri wa mtundu womwewu kuti atetezedwe mokwanira.

Padakali pano, katemera wa AstraZeneca anatsala ochepa koma dziko la Malawi likuyembekezera kulandira katemera wina wa AstraZeneca mwezi uno wa August.

Anthu okwana 463,236 ndi omwe abayitsako katemera wa Corona mdziko muno.

 

Advertisement

One Comment

  1. Zaveka ….koma kod tikalandila katemera ameneyu ndiye kut tisiya kuvala ma mask kapena izi mukuti socail distance ‘zi?

Comments are closed.