Thupi la wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino a Saulos Chilima kuphatikiza matupi ena a anthu asanu ndi anayi omwe amwalira pa ngozi ya ndege yomwe yachitika Lolemba mu nkhalango ya Chikangawa m’boma la Mzimba lafika pa bwalo la ndege la Kumuzu International Airports(KIA) mzinda wa Lilongwe.
Matupiwa afika kudzera pa ndege za a silikari za dziko la Zambia ndipo matupiwa analandiridwa ndi mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera.
Asilikali a nkhondo a dziko lino komanso a polisi ndi omwe akhala akukhwimitsa chitetezo pa malopa.
Atafika matupiwa, asilikali anapanga perete ngati mwambo opereka ulemu kwa wachiwiri wa mtsogoleriyu.
Poyankhura pa bwalo la ndegeli, Pulesidenti wakale wa dziko lino a Joyce Banda wati ndi wokhudzika kwambiri kamba ka imfa yomwe yagwera dziko lino.
Mtsogoleri wa chipani cha People’s Development Party (PDP) a Kondwani Nankhumwa ati iwo ndi okhudzika ndi imfa ya wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino popeza anali m’modzi mwa a zawo kwambiri komanso amawatenga ngati m’bale wawo weniweni.
“Nyonga ndilibe, mphamvu ndilibe, ndine othodwa kwambiri chifukwa cha imfa ya a Saulos Klaus Chilima chifukwa pakuti anali mzanga kwambiri ndipo padakali pano sindingakwanitse kuyankha mafunso mwina kutsogoloku chifukwa sindikumvetsabe zonsezi,” iwo anatero.
Kupatura apo , nduna yofalitsa nkhani a Moses Mkukuyu ati zambiri zokhudzana ndi mwambo onse wa maliro anthu adikire uthenga kuchokera kwa a Chakwera.
Atsogoleri ochokera ku zipani yosiyanasiyana monga Alliance for Democracy (AFORD), People’s Party (PP), Malawi Congress Party (MCP) komanso United Transformation Movement ( UTM) anali nawo ku bwalo la ndege la KIA kulandira malirowa.
Padakali pano, a Chakwera akhazikitsa komiti yoyendetsa mwambo wa malirowa. Mwambo oyika m’manda anthuwa awulengezabe. Iyi ndi ngozi yoyamba ya ndege yokhudza m’modzi mwa atsogoleri a dziko lino.