Inoyi ndi nyengo yolira tiyeni tilemekeze potsata dongosolo – Bandawe 

Advertisement
Saulos Chilima

Professor Chiwoza Bandawe yemwe ndi psychologist wapempha a Malawi kuti alemekeze imfa yomwe yagwera dziko lonse ya wachiwiri wa mtsogoleri wa dziko lino a Saulos Chilima komanso anthu ena asanu ndi anayi omwe amwalira pa ngozi ya ndege yomwe yachitika dzulo mu nkhalango ya Chikangawa m’boma la Mzimba.

Bandawe wayankhura izi pamene dziko la Malawi lili pa chisoni kamba ka imfa ya a Chilima ,a Patricia Shanil Dzimbiri amene anali mkazi wa Pulesidenti wakale a Bakili Muluzi komanso anthu ena asanu ndi atatu omwe anali mu ndegeyi. 

Poyankhura ndi kanema wa Zodiak, iwo ati ngakhale imfayi yapangitsa anthu kukhala ndi mafunso komanso kufuna kudziwa zambiri pa nkhani yangoyi, ati ndikwabwino kuti nyengo ino ikhale yolira chabe osati yoyankhura zinthu zosiyanasiyana. 

Bandawe adawonjezera ponena kuti a ndale onse kuchokera ku zipani zosiyanasiyana akuyenera kugwirana manja pamene dziko lino likukhunza imfayi.

“Pamene dziko lino lagweredwa imfa yotere tikuyenera kukhala anthu ambumba imodzi ngati dziko.Tikudziwa kuti tidzimva zinthu zambiri kuchokera kwa anthu osiyanasiyana komano padakali pano tikuyenera kutsatira uthenga kuchokera ku boma osati uthenga uliwonse kuchokera pa matsamba a mchezo,” atero a Bandawe.

Iwo ati anthu achepetse kukhala pamasamba a m’chezo ndiponso asamagotumizirana zinthunzi zilizonse chifukwa zibweretsa mafunso komanso malingariro ambiri potengera nyengo yomwe dziko lino likudutsamo. 

Professor Bandawe ati aMalawi akuyeneranso kuzindikira kuti imfa yomwe yagwera dziko lino yakhunza mawanja aanthu ambiri choncho anthu sakuyenera kutengera kuti poti ngozi siyikuwakhunza ndiye azingofalitsa zinthu yosiyanasiyana kutero ndikulakwa komanso kusowa umunthu. 

Pakadali pano, ma tupi anthu wa anyamulidwa pa ndege kupita ku Lilongwe komwe akalandiridwe ndi mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera.

Mwambo oyika m’manda anthuwa awulengezabe. Iyi ndi ngozi yoyamba ya ndege yokhudza m’modzi mwa atsogoleri a dziko lino.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.