Omenyera ufulu Bon Kalindo, wayamba kuchotsera milandu yomwe akuzengedwa pomwe khothi ku Zomba lalamura kuti nkuluyu ndi mfulu pa mlandu oyambitsa zipolowe omwe amazengedwa m’bomalo.
A Kalindo omweso amatchuka ndi dzina lawo la pazisudzo la Winiko, anamangidwa m’bomali pa 23 November chaka chatha pomwe zionetsero zomwe anatsogolera m”boma la Zomba zinathera zipolowe.
M’mwezi wa January chaka chino, khothi linapeze kuti a Kalindo akuyenera kuyankha mlandu oyambitsa zipolowe pa zionetsero zomwe iwo anatsogolera nthawi imeneyo.
Mbuyomu, mbali ya boma idabweretsa mboni zisanu m’bwalo la milandu ndipo mboni zinayi adali apolisi omwe amafufuza zamilandu yawupandu ndipo mboni imodzi adali mkulu yemwe amagwila ntchito pamalo ogulitsira zokumwa a Kangaroo ku Chinamwali.
Mkulu waku malo ogulitsira chakumwayu anauza bwalo la milanduli kuti katundu wa ndalama pafupifupi 8 million kwacha adabedwa ndi anthu osadziwika patsiku laziwonetsero zomwe a Kalindo ankatsogolera.
Koma popeleka chigulo za nkhaniyi, Principal Resident Magistrate Martin Chipofya wati potsatira kumva maumboni a mbali zonse ziwiri, a Kalindo sadalakwe kali konse.
Chipofya wati umboni wa mbali ya boma sunali wogwira mtima kuyelekeza ndi umboni watchutchu womwe mbali ya a Kalindo idapeleka m’bwalo la milandu.
Zatelemu chiwerengero cha milandu yomwe a Kalindo akuyankha chachepelako. Iye akuyankhaso mlandu onga omwewu m’boma la Mangochi komaso akuyankha milandu ina munzinda wa Lilongwe.