Gulu la anthu ogwira ntchito zaumoyo omwe sanalembedwebe ntchito, awopseza kuti apitilira ndi ganizo lawo lokasumira unduna wa zaumoyo pa zotsamwitsa zomwe zinachitika pa ndondomeko yolemba anthu ntchito ngati undunawu suwalemba ntchito nsanga.
Nkhaniyi inayamba mu February chaka chino pomwe unduna wa zaumoyo unatulutsa maina a ogwira ntchito zaumoyo omwe boma linawalemba ntchito m’magulu osiyanasiyana.
Potsatira kutulutsidwa kwa maina omwe analembedwa ntchitoyi, magulu osiyanasiyana a anthu mdziko muno anadzudzula undunawu kamba ka zolakwika zomwe zinakhudza ntchito yolemba anthuwa.
Undunawu ukudzudzulidwa kuti unalekelera kuti anthu osayenera apezeke nawo pa mndanda wa anthu omwe analembedwa ntchito ndipo anthu ena akuganizira kuti panachitika za chinyengo.
Utamva madandaulowa, unduna wa zaumoyowu kumayambiliro kwa mwezi uno unayamba kukoza zovuta zomwe zinalipo pa kalembedwe ka anthuwa, ndipo mwazina unatulutsa mayina olowa m’malo mwa anthu omwe anali osayenera kulembedwa ntchito.
Koma gulu la ogwira ntchito zaumoyo omwe sanalembedweso ntchito ulendo wachiwiriwu, lawopsyeza kuti ngati nawo salembedwa ntchito akasumira undunawu kamba kazolakwika zonse zomwe zinachitika.
Angapo mwa okhudzidwawa omwe anasankha kuti tisawatchule, ati iwo ndiodwabwa kuti undunawu unasankha kulemba ntchito magulu ochepa ena ndikuwasiya zomwe anati akuona kuti sizabwino.
Anthuwa ati pano akupanga chikozero choti apitilire ndi chilinganizo chawo chotengera nkhaniyi ku bwalo la milandu kuti akalamure kuti ntchito yolemba anthuyi iyambileso.
“Nde ma cardres amene tasala tilipo ochepa kwambiri chifukwa chani sanatipange include mu list atulutsa ija? Is it kuti ma cardres enawa ngopanda ntchito? Anangoti for other cardres it’s still underway if they have a reserve list zikuvuta pati kutulutsa list inayo mpaka itenge nthawi yonseyi?” Wadabwa munthuyo.
Munthu winaso mugululi watiuza kuti akuganiza kuti pali akuluakulu ena ku undunawu omwe akukhudzidwa komaso anapindulapo pa zolakwika zomwe zinachitikazi.
“Mwina pali munthu wina yemwe akumatenga malipilo a anthu omwe sanawapange replace that’s why akuzichedwetsa kwambiri sinnanga inali funding. Ngati ministry siyitulutsa list ina mwachangu nafeso tipita ku court to question the whole recruitment process,” watelo munthu wina.
Munthuyo watitsinaso khutu kuti pali mphekesera yoti anthu ena omwe analembedwa ntchito mosatsata malamulo, ayamba kale kupita ku ntchito zomwe ati zikuwapatsa chikaikiro ngati undunawu ukufunadi kukoza zolakwika zomwe zinachitikazi.
Ena mwa ma gulu a anthu ogwira ntchito zaumoyo omwe undunawu unalonjeza kuti ulemba anthu ake mu ndondomeko yokoza zolakwika zomwe zinachitikazi, ndi monga Optometry komaso Lab tecnologist kungotchulapo ochepa chabe