Potsatira kalata yomwe Zani Challe anatulutsa yodandaula komaso kuopseza kuti apanga chinthu china chomwe sananene pa Tuno kamba komunena kuti iye amagulitsa thupi komaso amachita malonda a mankhwala ozunguza ubongo, oyimbayu wapepesa tsopano.
Nkhaniyi inayamba Lachiwiri usiku pomwe oyimba Tuno yemwe anabadwa Tunosiwe Mwakalinga amacheza mu pologalamu ya ‘Truth or Drink’ yomwe limapangitsa ndi gulu la Madness Entertainment ndipo imaikidwa pa intaneti.
Mwazina Tuno anati Zani Challe asiye kumanena kuti kunja komwe ali pano akuyimilira oyimba akazi m’dziko muno ponena kuti kumeneko amapanga zinthu zosakhala bwino zomwe anati ndikuphatikizapo ku gulitsa thupi lake kwa azibambo osiyanasiyana.
Pomwe amapitilira kucheza mu pologalamuyi, Tuno anamutukwana Challe ati kamba komunena kuti iyeyo ndi Temwah samatha kuimba komaso kuti Tuno-yo akuti samatchena, ndipo apapa mpomwe anaonjezera kutsotsomora moto omwe unatentha mtima wa Challe.
“Ngati wapita ku Nigeria bwanji sindinakuone ndi Tiwa Savege. Unapita ku Nigeria kukatani iwe, ungamatinene kuti ine ndi Temwa kuti sititchena f*? Nde komwe wapitako umakapanga chiyani kumeneko,” anatelo Tuno kwinaku akugwilidwa, kuletsedwa kuti asapitilize kuyankhula.
Kupatula apo, Tuno anamunena Challe kuti m’mayiko akunja omwe amapita amakachita malonda ogulitsa mankhwala ozunguza ubongo zomwe zinapangitsa kuti Challe apse mtima kwambiri mpaka kufika potulutsa chikalata chomuopseza Tuno kuti apanga chinthu china ngati sabweretsa umboni wa zomwe amayankhulazo kapena ngati sapepesa.
“Ndine wokhudzidwa kwambiri ndi khalidwe losayenera limene munthu wina wachita, makamaka pondinamizira zinthu, kuphatikizapo bodza loti ndimachita nawo zinthu zosayenera monga kugulitsa mankhwala osokoneza ubongo ndi ntchito zoperekeza anthu.
“Ndikulimbikitsa munthu uyu kuti apereke umboni weniweni wotsimikizira zomwe akunena kapena kupepesa pagulu. Kulephera kutero kuchititsa kuti ndi chitepo kanthu. Ndikofunika kuzindikira kuopsa kwa mawu achidani, ziwopsezo za nkhanza zakuthupi, ndi kunene zopanda pake, popeza siziyenera kuonedwa mopepuka,” anatelo Challe mu kalatayo.
Podziwa kuti nkhondo siimanga mudzi, patangodutsa maola ochepa chitulutsileni kalatayo, oyimba Tuno naye sanazengeleze koma kutulutsaso kalata yake yomupepesa Challe pa zomwe iye anayankhula pomwe amajambulidwa kanemayo.
Mu kalatayi, Tuno sanayankhule zambiri koma wati akupepesa kuchokera pansi pa mtima ndipo wati wachotsa zonse zomwe analankhula pomwe amajambulidwa kanemayo yemwe anthu akumugawana kwambiri makamaka mbali yomwe Tuno anayankhula zonyoza Challe komaso oyimba ena.
“Ndatenga mphindi ino kupepesa kwa Zani Challe chifukwa cha ndemanga zomwe ndidalankhula za iye pa podcast ya “Truth of Drink”. Ndawachotsa mawuwa mu uthunthu wawo,” watelo Tuno mu kalata yopepesa Challe.
Tuno asanapepese anali atayamba kale kunong’oneza bondo pa zomwe anayankhulazo kamba koti m’mawa wa Lachitatu, analemba pa tsamba lake la fesibuku ndikunena kuti sali okondwa ndi zomwe anachita atamwa mowa mu pologalamuyi.
Iye anaonetsa kukhumudwa kuti atamwa mowa mu pologalamuyi anayamba kutukwana ndi kunyoza anthu ena osalakwa kuphatikizapo Challe zomwe anati ndi chisonyezo kuti iyeyo mowa si mbali yake ndipo akauyenera kusiya kumwa.