Mtsogoleri otsutsa boma mu nyumba ya malamulo yemwenso ndi mkulu wa amai mu chipani cha DPP, Mai Mary Navicha, wati amai ambiri apangidwa chipongwe powagwirira pa chipolowe chomwe chinali dzulo mu mzinda wa Lilongwe.
Dzulo chipanichi chinali ndi ndawala yomeneza anthu kuti akalembetse cha unzika pokozekera chisankho cha 2025 koma anthu ena anabwera ndikukhapa anthu komanso kuphwanya magalimoto.
A Navicha ati amai ena angwililiridwa ndipo apempha mabungwe oyang’anira za malamulo m’dziko muno kuti alowelerepo ndipo chilungamo chioneke poyera chifukwa mchitidwewu ukapitilira pali chiopsezo choti amai ambiri sadzitenga nawo gawo pa ndale.
“Ngakhale chiwerengero cha amene achitilidwa chipongwe chi sitinachipeze koma tikhulupirira kuti izi zinakonzedwa ndi chipani cha Malawi Congress Party (MCP),” atero a Navicha.
Mu chikalata chomwe watulutsa mpingo wa CCAP, sinodi ya Blantyre kudzera kwa M’busa Master Jumbe komaso Mathews Kajani, chikufunsa apolisi kuti afufuze omwe anayambitsa chipolowechi.
Pakadali pano, mneneri wa chipani cha MCP, Ezekiel Ching’oma watsutsa ganizo loti chipolowechi anapanga ndi a MCP ndipo mneneri wa apolisi m’dziko muno, Peter Kayala wati apolisi afufuza omwe apanga upanduwu.
Wolemba: Peter Mavuto