Boma lati ntchito yomanga mabwalo a Bullets ndi Wanderers iyambilaso

Advertisement
Part of the game between Nyasa Big Bullets and Mighty Wanderers

Boma kudzera ku ndondomeko ya za chuma cha dziko lino ya chaka cha 2024/2025 laika ndalama zoyambilaso ntchito yomanga bwalo la zamasewero a matimu a FCB Nyasa Big Bullets komanso Mighty Mukuru wanderers.

Ntchitoyi inaima miyezi nkhumi ndi iwiri yapita kamba kosowa ndalama.

Malinga ndi ndondomeko ya za chuma yomwe unduna wa za chuma watulutsa, ndalama zokwana K1.5 biliyoni ndi zomwe zigwire ntchito yomanga ma bwalo a za masewero a matimu awiriwa komanso Mzuzu Youth Centre.

Boma laikanso ndalama yokwana K1.8 biliyoni kuti igwile ntchito yomanga  Griffin Saenda Indoor Sports Complex ndi National Aquatic Complex pamene K464 miliyoni ndi yomwe igwire ntchito yokonzaso Bwalo la Bingu mu mzinda wa Lilongwe ndipo K80 miliyoni igwira ntchito yokonzaso Bwalo la Kamuzu mu mzinda wa Blantyre.

Wolemba : Peter Mavuto

Advertisement