Tiyeni tipempherere mvula, latero bungwe la EAM

Advertisement

Bungwe la Evangelical Association of Malawi (EAM) lapempha anthu onse dziko muno kuti pakhale mapemphero apaderadera opemphelera mvula kamba ka ng’amba yomwe yakhudza m’dera ambiri m’dziko muno.

Chikalata chomwe wasainira ndi mlembi wamkulu m’bungweli, M’busa Francis Mkandawire,   chikumeneza anthu onse dziko muno posatengera chipembedzo kutenga nawo gawo mapempherowa kuti mvuLa iyambeso kugwa moyenera.

“Tipempere ma nyumba, Malo athu opembedzera ndi ku Malo athu a ntchito ndipo amene tingathe kusala ndi ku pemphera tikulimbikitsa kutero,” Mbali imodzi ya chikalatachi yatero.

Mapempherowa akhazikitsidwa kuyambira pa 11 February, 2024 mpaka mtsogolomu.

Kuyambira chaka chatha, nthambi yoona za nyengo dziko muno yakhala ikulosera ng’amba yomwe ikukhudza m’dera ambiri ndipo mbeu zina zayamba kale kuuma kamba ka vutoli.

Advertisement