Akathyali atatu awanjata kamba koyendetsa champeni lamya za anamfedwa pamaliro

Advertisement

Akathyali atatu akhwidzingidwa ndi apolisi ku Lilongwe kaamba kowaganizira kuti adayendetsa champeni (kuba) lamya za m’manja za anafedwa pamaliro dzulo m’mudzi wa Kamganga kwa mfumu yaikulu Mavwere m’boma la Mchinji.

Nkhani yonse ikuti akathyali atatuwa omwe mayina awo ndi a Steven Mofolo azaka 31, a Andrew Manase azaka 28 komanso a Innocent Phiri azaka 33, dzulo lachinayi akathyaliwa adabera anamfedwa lamya za m’manja pamaliro.

Apolisi owona zofufuzafufuza ochokera ku nthambi yaying’ono ya Chitipi anakwanitsa kunjata akathyali atatuwa pa chipatala chachikulu cha Kamuzu Central Hospital, ndikusokolotsanso ma lamya anayi komanso kachipangizo kosungiramo mphamvu zamagetsi pachingerezi (power bank).

Malingana ndi mneneri wa apolisi a Constable Khumbo Sanyiwa wati akathyali atatuwa pompano akaonekera ku bwalo la milandu komwe akayankhe pa mlandu okuba katundu.

A Innocent Phiri, ndi am’mudzi mwa Chilumba kwa mfumu yaikulu Msamala ku Balaka, Andrew Manase amachokera m’mudzi mwa Gowelo, kwa mfumu yaikulu Chikumbu m’boma la Mulanje, pamene a Steven Mofolo amachokera m’mudzi mwa Ngulanga, kwa Likoswe ku Chiradzulu.

Wolemba: Ben Bongololo

Advertisement