Mutharika wati MCP ikukoza zodzabera chisankho

Advertisement
Peter Mutharika

Mtsogoleri wakale wa dziko lino a Peter Mutharika ati chipani cha Malawi Congress Party (MCP) chikukonza zoti chidzabele chisankho chosakha mtsogoleri wa dziko cha chaka cha mawa. 

A Mutharika amayankhula izi Lamulungu pa Njamba munzinda wa Blantyre pomwe chipani chawo cha Democratic Progressive Party (DPP) chinachititsa nsonkhano wa ndale. 

Poyankhula ku khwimbi la anthu lomwe linasonkhana pa malowa, a Mutharika omwe anthu owanyadira amawatchula kuti “a Dad”, ati amvetsedwa kuti chipani cha MCP chikuphika ma pulani oti chidzabele chisankho chikudzachi. 

Mwa zina, iwo ati pakalembera wa unzika yemwe akuchitika pano, chipani cha MCP chikufuna kulembetsa anthu okwana 1 miliyoni ochokera m’dziko la Mozambique kuti adzavote nawo pachisankhochi komanso ati chipanichi chikupanganso upo ndi mpingo wina. 

“Ndikudziwa kuti ali ndi ma pulani osiyanasiyana ofuna kubera zisankho za 2025. Akufuna alembe anthu okwana 1 miliyoni kuchokera ku Mozambique kuti adzavote nawo komanso pali mpingo umodzi omwe akufuna kuti ulembetse anthu 500,000. 

“Ndavanso kuti akadzaluza pa 2025 pano sadzavomerayi. Koma ndiwauze, ndiwachenjeze kuti akazakana zotsatira za chisankho ife titawina mhm,” watelo Mutharika. 

Mtsogoleri opumayi watinso chipani cha MCP chikukoza zosokoneza ntchito yolembetsa ziphaso zaunzika mchigawo cha kumwera komanso kumpoto kuti muzigawozi anthu asalembetse ochuluka kuyerekeza ndi chi gawo cha pakati. 

Pamavuto omwe anthu akukumana nawo mdziko muno, Mutharika wauza a Malawi kuti asadele nkhawa kamba koti iwo pamodzi ndi chipani cha DPP akubweraso kudzawombora dziko lino ndipo watsindika kuti adzakoza zinthu mu zaka ziwiri zokha. 

“Ine ndikulonjeza kuti mu zaka ziwiri zokha ndizakoza dziko lino. Choncho ine ndi kuti musakhumudwe chi thandizo chikubwera chifukwa ife tikubweranso m’boma. Ine ndikuimanso chifukwa dziko lino lawonongeka. 

“Ndikubwera kuti ndidzapulumutse dziko lino. Muno m’dziko la Malawi muli mavuto ambiri ndipo a Tonse Alliance yabweretsa mavuto ochuluka. Zinthu zambiri zakwera chifukwa cha Chakwera,” watelo Mutharika. 

Iye anatsendera ndikulangiza otsatira chipani cha DPP kuti akhale ogwirizana, osachitirana nsanje ndicholinga choti loto lawo lobweleranso m’boma litheke mosavuta.

Advertisement

One Comment

  1. Sizinakukwaneni zomwe munaba zija. Mwauponda ulendo uno mpeza akubanja anu basi

Comments are closed.