Zidzukulu zanjatwa popha gogo wawo pa nkhani za ufiti


Zaka zapitazo Gogo Elisa Supuni ya zaka 73 m’boma la Mulanje inabala ana, ndipo ana awowo anabalaso ana, koma mphuno salota gogowa sanadziwe kuti adzaphedwa ngati njoka ndi zidzukulu zawozi powaganizira kuti gogowa anapha m’matsenga chidzukulu chawo china.

Tikukukamba pano zidzukulu zitatu zili m’manja mwa apolisi.

Watsimikiza za kumangidwa kwa zidzukuluzi ndi ofalitsa nkhani pa polisi ya Mulanje a Innocent Moses ndipo wazindikira atatuwa ngati a Bauleni Chipangula, a zaka 23, Martin Misomali, a zaka 19 ndi Dalitso Misomali, a zaka 21, onse a m’mudzi mwa Thigira mfumu yaikulu Njema m’bomalo.

A Moses ati atatuwa amangidwa chifukwa chopha agogo awo a Supuni pa 21 December, 2023 potsatira imfa ya Ellen Chipangula yemwe anali mchemwali wa oganizilidwawa ndipo anamwalira atadwala kwa nthawi yaitali.

Apolisi ati Chipangula anadwala kwa nthawi yaitali ndipo pa 7 December, 2023, anachitidwa opaleshoni ya pamimba pa chipatala cha boma cha Mulanje koma pa 21 December, 2023 anamwalira zomwe sizinasangalatse achibale ake ena kuphatikiza oganizilidwawa.

Ofalitsa nkhani za polisi ya Mulanje-yu wati zitangodziwika kuti Chipangula wamwalira, zidzukulu zitatuzi kuphatikizaposo achibale awo ena angapo, anathamangira kwa gogo Supuni ndikuyamba kuwamenya powaganizira kuti ndiomwe apha nsungwanayo m’matsenga.

Gogo Supuni anavulazidwa kwambiri ndipo anamwalira tsiku lomwelo pomwe anatengeledwa ku chipatala cha Namasalima ndipo nkhaniyi itatengeledwa ku polisi, achitetezowa anakhazikitsa kafukufuku wawo yemwe zotsatira zake ndikuphatikiza kumangidwa kwa makosana atatuwa.

Atatuwa akuyembekezeka kukaonekera ku bwalo la milandu kafukufuku wa apolisi pa nkhaniyi akamalizika komwe akuyenera kukayankha mlandu wakupha munthu.