Agamulidwa kukakhala ku ndende kaamba koseweletsa maliseche a msungwana wachichepere

Advertisement

Bwalo la milandu ku Balaka, lagamula bambo wa zaka 59 zakubadwa a Steven Finye kukakhala ku ndende komanso kugagwira ntchito ya kalavula gaga kwa zaka ziwiri kaamba kopezeka olakwa pa mlandu oseweletsa maliseche a msungwana wa zaka zisanu ndi zinayi (9).

Malingana ndi chikalata chochokera ku Polisi ya Balaka chomwe wasainila ndi wachiwiri kwa ofalitsa nkhani za polisi m’bomali, Seargent Mphatso Munthali chati oimira boma pa milandu Superitendent Bodwin Msukwa adauza bwalo la milandu kuti bamboyu adapalamula mlanduwu pa 7 March chaka chomwechino.

A Msukwa adati mtsikanayu adatumidwa kunyumba kwa mkulu opalamula mlanduyu kukafunsa ngati akazi ake adali atakonzeka pa ulendo wopita ku maliro. Msungwanayu akuti adalandilidwa ndi bambo wa chimasomasoyu yemwe adayamba kuseweletsa maliseche a mwanayu asanamukakamize kuti nayenso agwile komanso kuseweletsa chida cha bamboyu.

Msungwanayu atabwelera kunyumba kwawo adakanena kwa mai ake za malodzazi ndipo mai akewo sadachedwe kukanena ku police zomwe zidapangitsa kuti apolisi akwizinge bamboyu ndi unyolo.

Ndipo powonekera mu bwalo la milandu, oyankha mulanduyu adavomera mulandu omwe amazengedwa zomwe ndi zosemphana ndi gawo 160 la malamulo oyendetsera dziko lino.

Iwo adapempha bwalori kuti liwafewetsele chilango kaamba koti ndi akulu komanso akudwala. Koma oimira boma pa mlanduwu, a Msukwa adapempha bwalori kuti lipeleke chilango chokhwima kwa njondayi Kamba koti kutengera ndi zaka zake, njondayi idakatha kupewa kupalamula mulanduwu.

Ndipo mu chigamulo chake, oweruza milandu a Joshua Nkhono adagwilizana ndi a Msukwa ndipo adalamula kuti njondayi ikakhale ku ndende komanso kugwira ntchito ya kalavulagaga kwa zaka ziwiri kuti anthu ena a maganizo onga awa atengelepo phunziro.
Njondayi imachokera m’mudzi mwa Masende , mfumu yaikulu Chigalu m’boma la Blantyre.

Advertisement