La fote limakwanabe, Bambo ku Kasungu anjatidwa atabvulidwa chigoba

Advertisement

Bambo wa zaka 23, ali m’chitokosi cha apolisi m’boma la Kasungu pomwe akuyembekezeleka kuyankha mlandu ofuna kuba mu dzina la polisi.

Bamboyu yemwe dzina lake ndi Lonjezo Banda, wagwidwa usiku wa lachinayi akufuna kulanda njinga za moto kwa oyendetsa kabaza ponamizila kuti iyeyo ndi polisi ofisala.

Pamodzi ndi nzawo wina, ma lipoti akuti bambo Banda anatchinga nsewu pafupi ndi sukulu ya nkomba phala ya Merat atabvala makaka a kamofoleji  ndipo amakakamiza  woyendetsa kabaza kuti apereke ndalama kuti aombole njinga zawo.

Wachiwiri kwa wofalitsa nkhani za polisi m’bomali, a Miracle Hauli, wati  m’modzi  mwa oyendetsa kabaza wa njinga ya moto, bambo Kamlepo Saka,  anathawa posayimira zigawenga ziwirizo ndipo anakamema anthu ena kubwera kuzagwira a Banda.

Nzawo wa a Banda m’chiwembuchi  anakwanitsa kuthawa atamupeza ndi mpeni wakuthwa ndi nyundo.

A Banda  akaonekela ku bwalo la milandu posachedwapa kukayankha milandu apezeka nayo.

Nkhaniyi ikudza pamene m’chitidiwe okuba mu dzina la polisi ukuchulukira m’dziko muno. 

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.