Mphatso: Khothi lamasula mtsikana opha mwana wake

Advertisement
Mphatso Kaonga was represented by the Legal Aid Bureau

Mtsikana wazaka 20 yemwe anamangidwa mu 2021 kamba kakupha “mwangozi” mwana wake wa chaka chimodzi ndi miyezi 9, lero ali ndi chimwemwe chodzadza tsaya pomwe wamasulidwa ndipo wauzidwa kuti asapalamuleso mlandu uli onse kwa chaka chimodzi.

Mtsikanayu yemwe dzina lake ndi Mphatso Kaonga ochokera ku Nthalire m’boma la Chitipa, anamangidwa ali ndi zaka 18 pomuganizira kuti adapha mwana wake wa miyezi 21, ndipo amazengedwa mlanduwu ngati mwana.

Malingana ndi tsamba la fesibuku la bungwe loyimilira anthu pa milandu mwaulele la Legal Aid Bureau, Mphatso adatenga pakati ali ndi zaka 17 koma pa nthawiyi sadadziwe yemwe adamupatsa pakatipo ndipo tsiku lina mwana atabadwa, anatenga mwana wakeyo ndikumupha “mwangozi” zomwe zinapangitsa kuti amangidwe ndi apolisi m’bomali.

Legal Aid Bureau yomweso inamuyimilira mtsikanayu pa mlanduwu, yati Mphatso ataonekera ku bwalo la milandu miyezi yambuyoyi, adavomera mlanduwu ndipo amasungidwa pa ndende ya Chitipa kudikira kuti adzapatsidwe chigamulo.

Bungweli lati zikuoneka kuti Mphatso anapha mwana wake “mwangozi” kamba koti pa nthawi yomwe izi zinkachitika, panali zisonyezo zoti mtsikanayu anali akudwala matenda akusokonekera kwa mutu ndipo akuti iye anauza bungweli kuti m’mbuyomu adadwalapo malungo othamangira ku bongo zomwe zidachititsa kuti asiye sukulu kaamba kosokonekera m’maganizo.

Potsatira mfundo zomwe bungwe la Legal Aid Bureau linapeleka ku khothi zomwe ndikuphatikizapo uchichepele wa mtsikanayu komaso kusayenda bwino kwa mutu wake pa nthawi yopalamula mlandu, oweruza milandu Justice Justuce Kishindo sanachitile mwina koma kumuuza mphatso kuti ndi mfulu tsopano.

Oweruza milanduyu wauza mtsikanayu yemwe anakhetsa msozi wa chimwemwe kuti awonetsetse kuti asapalamule mlandu uli onse pa miyezi khumi ndi iwiri (12) ikubwerayi.

Advertisement