A Malawi ayembekezere kupitilira kukwera kwa mitengo ya zinthu, watero Katswiri pa zachuma


Dr Betchani Tchereni is a Malawia economist and pundit who provides opinions on economic issues

Pamene dziko la Malawi likupitilira kukumana ndi mavuto osiyanasiyana pankhani yokhudza zachuma, katswiri pa nkhani ya zachuma a Betchani Tchereni wawuza a Malawi kuti ayembekezere kuti pali kuthekera koti mitengo ya zinthu pa msika ipitilira kukwera.

Malingana ndi a Tchereni, izi zikuyenera kuchitika chonchi pamene ndalama ya dziko lino sinakhazikikebe pa msika.

Iwo anapitilizanso kunena kuti ndalama ya kwacha ikadzakhazikika ndi pamene mitengo ya pa msika idzakhazikike.

Iwo anati vutoli ndi chifukwa cha kugwetsa mphamvu kwa ndalama ya kwacha ndi 44 pelesenti komwe kudachitika kumayambiliro kwa mwezi watha mu Novembala.

A Tchereni anatinso ngakhale izi zili chonchi, kugwetsa kwa ndalama yakwacha kuli ndi ubwino ndipo a Malawi akuyembekezereka kusimba lokoma ndalamayi ikakhazikika.