…akuti samapanga chibwezi ndi azibambo obowoka mthumba
Pomwe amayi oyendayenda ena akumatchaja ma K1000 komanso ma K2000 m’makwalalamu, oyimba wankazi otchuka m’dziko muno Zani Michelle Chiumia yemwe amatchuka ndi dzina loti Zani Challe, watutumutsa abambo omwe amamufuna pomwe waulura kuti ofuna kuchita naye ga! Ga! Ga! akuyenera kutulutsa ndalama yosachepera 20,000 ya ku America yomwe ndi pafupifupi 34 miliyoni kwacha.
Zani Challe amayankhula izi lachiwiri pa 5 December pomwe amacheza mu pologalamu yotchedwa ‘Truth or Drink’ ya kanema wa pa intaneti yomwe ikutchedwa ‘Madness Entertainment’.
Mkatikati mwa pologalamuyi, Zani Challe anafusidwa kuti afotokoze ngati anapatsidwapo ndalama kuti agonane ndi munthu ndipo m’maso muli mbee, oyimbayu anayankha mosapsatira kuti eya anapangangako mu njira yoti amayenda ndi amuna a ndalama.
Apa nyenyeziyi inapitilira ndikufotokoza kuti itha kulora kugonana ndi mwamuna aliyese koma wanenetsa kuti izi amapanga pokhapokha ndalama yomwe mamunayo akupeleka ikhale ya ndii koma wati iye simzimayi ogulitsa thupi.
“Nditha kugona ndi mamuna ngati mtengo wake uli oyenera. Mtengo oyenera ndi 20,000 USD (pafupifupi 34 miliyoni kwacha). Koma sizikutanthauza kuti ndine hule. Choyambilira ndikuyenera mamunayo ndimukonde kaye. Ineyo sindipanga chibwezi ndi azibambo opanda ndalama.
“Azibambo omwe ndimawakonda ndi okhawo omwe atha kunditumizira ndalama ngati 20,000 USD, atha kunditengera kunja pa ndege, kunditengera kokashopa. Koma sikuti ndine hule,” watelo Zani Challe.
Oyimbayi yemwe akuti ali ndi zaka 35, wati amakhumbira kudzakhala ndi ana anayi (4) koma wati pano alibe mwana ngakhale m’modzi kamba koti wati sanapeze wa chikondi okhazikika.
Nkhani ya 34 miliyoni kwacha yadzetsa mapokoso m’masamba anchezo ochuluka kamba koti anthu ena akuti mkaziyu wakokomeza kwambiri ndipo ena akuti palibe mamunayo amene angapeleke ndalama yochuluka choncho kwa mkazi kuti angogone naye basi.