Atupele wapepesa mavenda okhudzidwa ndi ngozi yamoto ku Zomba

Advertisement
Zomba Market Fire affected person

Mmodzi mwa akuluakulu a chipani cha United Democratic Front UDF Atupele Muluzi wapereka thandizo la ndalama yokwana K200,000 anthu omwe anakhudzidwa ndi ngozi ya moto mu nsika waukulu wa Zomba.

A Muluzi apereka thandizoli kudzera Kwa mfumu ya mzinda wa Zomba Khansala Davie Maunde yomwenso yapempha anthu ena akufuna kwabwino kuti athandize anthu omwe akhudzidwa ndi ngoziyi.

Khansala Maunde wati chipani cha UDF ndichokhudzidwa ndi ngozi yamotoyo ndipo wati mchifukwa chake wolemekedzeka a Muluzi aganiza zopereka thandindzo la ndalamazo kuti mavenda omwe akhudzidwa ndi ngoziyo apeze poyambira.

Pamenepa Khansala Maunde adathokoza wolemekezeka a Atupele Muluzi chifukwa chobwera mwachangu kudzathandiza ndi ndalama kwa mavenda okhudzidwawo ndipo adati izi ndizomwe zimafunika pachikhalidwe chathu.

“Tiyamikile nduna yoona za maboma ang’ono popereka thandizo Kwa anthuwa dzulo koma mkofunikabe anthu apitilize kupeleka thandizo,” anafotokoza a Maunde.

Lowereku madzulo moto udagwira shopu ya a James Kanjinga mu msika waukulu wa Zomba ndipo katundu wandalama zankhani nkhani adawonongeka komanso mavenda ena omwe ayandikana ndi shopuyi katundu wao adabedwa ndi anthu osadziwika omwe amathandidza kuchotsa katundu kuti asawonongeke ndi motowo.

Advertisement

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.