Ogwililira mwana wake omupeza agamulidwa kukakhala ku ndende zaka zisanu ndi chimodzi

Advertisement

Bwalo lozenga milandu ku Balaka lagamula bambo wa zaka 23 zakubadwa, a Thomas Kanyimbo, kugagwira ntchito ya kalavulagaga  ku ndende kwa zaka zisanu ndi chimodzi (6) kaamba kopezeka olakwa pa mlandu ogwililira mwana wake omupeza wa zaka zisanu ndi ziwiri (7).

Oimira boma pa milandu, Sub Inspector Liston Sabola, adauza bwalo la milandu kuti bamboyu adapalamula mlanduwu pa 18 February chaka chomwe chino m’mudzi mwa Kanono omwe uli m’malire a maboma a Balaka ndi Neno.

A Sabola adauzaso bwalori kuti pa zifukwa zina, bamboyu  amakhala nyumba zosiyana ndi mkazi wake omwe ndi mai ake a mwana ochitilidwa nkhanzayu.

Tsopano chomwe chidatsitsa dzaye kuti njobvu ithyoke nyanga ndi chakuti mkatikati mwa usiku wa tsikuli, bambo wa maso m’mwambayu adazembera mwanayu kuchipinda komwe amagona ndipo adamuvula zovala zake ndi kuyamba kumugwililira.

Komatu mwanayu adakanika kukuwa kuti anthu amupulumutse ku malodzawa kamba kakuti bamboyu adamutseka mwanayu pakamwa ndi manja ake zomwe zidamupangitsa kuti akanike kutulutsa mawu.

Bamboyu atakwanilitsa chilakolako chake adathawira ku malo osadziwika.

Msungwanayu atafotokozera mai ake za nkhaniyi, iwo adakatula nkhaniyi  kwa nyakwawa Kanono omwe adalangiza maiyu kuti akadandaule nkhaniyi ku polisi. Izitu zidapangitsa kuti apolisi ayambe ntchito yosakasaka bamboyu ndipo adakwanitsa kumugwira patapita masiku angapo.

Ndipo powonekera mu bwalo la milandu, bamboyu anakana mulandu omwe amazengedwa omwe ndi osemphana ndi gawo 138 la malamulo oyendetsera dziko lino. 

Izitu zinapangitsa mbali ya boma kuitanitsa mboni zisanu zomwe zidapelekera umboni osonyeza kuti njondayi idachitadi khalidwe lonyansali.

Komabe, njondayi idapempha bwaloli kuti limufewetsele chilango ponena kuti satana ndi yemwe adamupangitsa kuchita chakwaipachi.

Ndipo mu chigamulo chake, oweruza milandu a Majisitiliti Phillip Chibwana adakana kwa ntu wa galu pempho la bamboyu kuti amufewetsele chilango chifukwa adapalamula mulandu chifukwa cha mphamvu ya satana ndipo adalamula njondayi  kuti ikagwire ukaidi kwa zaka zisanu ndi chimodzi kuti anthu ena a maganizo ngati awa atengelepo phunziro.

A Kanyimbo amachokera m’mudzi mwa Kanono, mfumu yaikulu Symon m’boma la Neno.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.