Chizindikiro cha chipani chatsopano chiutsa mtsutso

Advertisement

Mtsutso wabuka pa masamba a nchezo pa nkhani ya chizindikiro cha chipani chomwe  changobadwa kumene cha People’s Development Party (PDP).

Chipanichi, chomwe mtsogoleri wake ndi membala wakale wa chipani cha  Democratic Progressive Party (DPP), Kondwani Nankhumwa, chagwiritsa ntchito mbalame ya Nkhwazi ngati chizindikiro chake.

Pomwe anthu ena sakuonapo vuto, ena akuti ma kampani ena amagwiritsa kale ntchito chizindikirochi kuphatikizapo polisi ya dziko lino.

Malingana ndi ndemanga zomwe taona m’masamba a nchezo a fesibuku komaso watsapu, anthu ati ali odabwa ndi chiganizo cha chipanichi.

“Komatu chi logo ichichi chili kale ndi eni ake. Mesa kampani inayake ya security imagwiritsa chomwechi? Komanso zasiyana pati ndi chi eagle cha Malawi police chija? Apapa sizinayende sure,” watelo munthu wina pa fesibuku.

Ngakhale kuti sizikudziwika kuti chizindikilochi chikutanthauzanji, munthu wina wati anakakonda chizindikilochi chitasinthidwa ponena kuti; “Mbalame iyi ndiyosakaza, yoononga ziweto ndipo yopanda chifundo, nde kaya mwina tidikile atiuze kuti ikutanthauza chiyani.”

Ngakhale zili chonchi, ena akuti sakuona vuto lili lonse ndi chizindikirochi ponena kuti chachikulu ndi nfundo zabwino zomwe zingathandizile kupititsa patsogolo dziko la Malawi.

“Inu zinazo zisiyeni ife chomwe tikufuna ndi kuti zinthu zisinthe m’dziko muno. Logo siyingatipatse chakudya. Nankhumwa tili pambuyo pano bwana,” watelo munthu wina poyikira ndemanga za nkhaniyi pa tsamba lathu la fesibuku.

Imodzi ya ma kampani amene ali ndi  chizindikiro chofanana ndi chipani cha PDP ndi Fast Security Solutions yomwe imagwira ntchito za chitetezo.

Kampaniyi yomwe inatsegulidwa mu chaka cha 2020, yatulutsa kalata yowuza anthu kuti kampaniyo isatengedwe ngati chipani cha ndale kamba kakufanana kwa chizindikiroku.

“Fast Security Solutions ikufuna kudziwitsa anthu onse kuti logo yomwe ili pamwambapa isasokonezedwe ndi logo ina ya chipani chilichonse mdziko muno. Fast Security Solutions ndi yodzipereka popereka chitetezo molingana ndi ziphaso zoyenera komanso zilolezo zomwe idalandira kuchokera ku boma la Malawi motero sichiyenera kutengedwa ngati chipani cha ndale ngakhale chipani cha ndale chitakhala ndi chizindikiro chofanana ndi cha Fast Security Solutions,” yatelo kampaniyo.

Pomwe pakhala pakuveka manong’onong’o kuti a Nankhumwa akuyambitsa chipani chawo, m’masamba nchezo mumayenda chizindikiro cha manja atatu ogwilana zomwe ndi zosiyana ndi chizindikiro chomwe chipanichi chatulutsa pakukhazikitsidwa kwake.

Pakadali pano a Nankhumwa, omwe ndi mkulu wa zipani zotsutsa boma kunyumba ya za malamulo, sanakambe kalikonse pa nkhaniyi.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.