Chakwera abowola mtambo kupita m’dziko la Kenya

Advertisement

Mtsogoleri wadziko lino a Lazarus Chakwera lero anyamuka kupita mdziko la Kenya komwe akakhale nawo pa msonkhano wa banki yayikulu yadziko lonse ya World Bank.

Mtsogoleriyu akuyembekezeka kudzanyamuka kudzera pabwalo la ndege la Kamuzu munzinda wa Lilongwe 1 koloko masana.

Msonkhanowu udzachitika Lolemba mumzinda wa Nairobi m’dzikolo. 

Mtsogoleriyu adzabwerela kuno ku mudzi lolemba lomwero kudzera pa bwalo la Kamuzu, nthawi ya 5 koloko madzulo.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.