A zaumoyo adandaula ndi kuchoka kwa MSF ku Chiradzulu

Advertisement
MSF phasing out its projects in Malawi

Mkulu oyang’anila zaumoyo m’boma la Chiradzulu Dr. Jamson Chausa wadandaula ndikuchepekedwa komwe kukhalepo pamene bungwe la Medicines San Frontiers (MSF) ikhale ikuchoka bomali.

Izi amayakhula pa mwambo osazikana ndi mafumu komanso ma khansala ndi adindo ena omwe MSF inakoza dzulo ku ma ofesi awo ku Chiradzulu.

Mwa zina iwo anati MSF yakhala ikuthandiza kwambiri kwa zaka 25 polimbana ndi matenda a HIV komanso umoyo wabwino kwa ana achichepele.

“Ngati Chiradzulu, ndife odandaula kwambiri kuti mukuchoka ndipo tukupemphani kuti mutigwilebe mkono komanso ngati mkotheka kutilumikizitsa ndi abale ena oti tizigwilanawobe ntchito yopitisa za umoyo patsogolo,” adatero a Chausa.

Koma poyakhapo a Chistine Wagari omwe amaona zamapulojekiti ku MSF m’Chiradzulu ati iwo akhalebe akuthandiza bomali kwa chaka chatunthu ndi makhwala komanso zipangizo za ndalama yosachepela K79 miliyoni kwacha.

Iye anathokoza mafumu komanso adindo ena a m’bomali kamba kogwila nawo ntchito kwa zaka zokwana 25.

Bungweli mwazina lakhala likupeleka thandizo la zakudya, mayendedwe ndi zina kwa ana omwe akhala akupezeka ndi matenda a HIV komanso lakhala likuchita zambiri kulimbikitsa za umoyo m’bomali.

Advertisement