A Malawi akunyinyilika Wode Maya atatchula mbewa kuti soseji

Advertisement
Wode Maya Malawi

Inde mlendo Wode Maya wadza nkalumo kakuthwa, komatu wadzetsa kung’ung’udza m’masamba anchezo pa mpanje pano kaamba koti waliuza dziko la pansi kuti ku Malawi kuno mbewa zija ndi makoswe komanso akuti ‘makoswewo’ timawatchula kuti soseji ya mu Africa.

Wode Maya yemwe dzina in a lake lenileni ndi Berthold Kobby Winkler Ackon ochokera m’dziko la Ghana, wakhala ali m’dziko muno kwa masiku angapo ndipo akuyenda malo osiyanasiyana, kusilira za chilebgedwe zomwe dziko la Malawi linadalitsika nazo.

Mkuluyu akumati akafika pa malo akumajambula makanema a malo omwe wafikawo kwinaku akuthyakula chingerezi choyamikira za chirengedwe zomwe dziko lino lili nazo komaso anthu ansangala omwe akumakuna nawo.

Wode Maya akumayika ma kanema akewo pa intaneti ndipo dziko la pansi ladziwa zinthu zochuluka za chilengedwe zomwe Malawi ali nazo ndipo a Malawi ochuluka akuyamikra mkuluyu kuti waligulitsa dziko lino pa nkhani ya zokopa alendo.

“Mkulu uyu Wode Maya waku Ghana koma ndiye waigulitsa Malawi. Wafika pena paliponse and anthu amaiko ambiri adziwa zambiri za Malawi,anthu ena marketing amaitha!!! Kuponda Salima, Nkhotakota, Mzuzu,Dowa paliponse.

“Kunena chilungamo kubwera kwa mkulu waku Ghana uyu, Wode Maya a Malawi ambiri tatseguka maso ndipo watiposa tivomereze. Malo ambiri wafikako iyeyu ambirife chibadwire sitinapondeko zina timangodzimvera mmabukhu koma kubwera kwa iyeyu tatha kuona maziko ambiri obisika mdziko mwathu muno.

“Mwachitsanzo timangomva za khumutcha Dr Napoleon Dzombe koma ma achievement awo tawadziwa pompano for example Kalipano Country Resort komanso nyanja yomwe anachita kukumba okha aaw beautiful,” wayamikira munthu wina pa fesibuku.

Koma zonsezo zili apo, Wode Maya wautsa mapokoso pa masamba anchezo kaamba koti nkatikati mwa maulendo ake m’dziko muno, anagula mbewa ndikujambulitsa zili pa mpani.

Mkuluyu anaika pa tsamba lake la thwita chothunzi atanyamula utaka fumbiwo kwinakuso atanyamula kaloti (carrot) ndipo analemba uthenga nchizungu omwe kutanthauzira kwake nkuti; “ku Malawi amazitchula kuti soseji ya mu Africa (makoswe).”

Mawuwa apangitsa kuti anthu amwere madzi zabwino zomwe Wodemaya wachita, ndipo ambiri akung’alura mkuluyu ponena kuti ndichipongwe chachikulu kuzitchula mbewa kuti ndi makoswe komaso kunena kuti a Malawi amawatchula ‘makoswewo’ kuti soseji ya mu African muno.

“Wode Maya, we need an apology. We don’t eat Rats and these are not Malawian (African) sausages, usatinyozese chonde chifukwa tipezeka tayamba kukun’galula nkuyiwala zabwino zonse zomwe wapanga, ife sitichedwa,” wadandaula munthu pa fesibuku.

Koma kung’ung’udzaku kuli apo, a Malawi ena akhalirana pa mtengo wa kachere ndikuyamba kulangizana kuti nkofunika kumatukulana okhaokha ponena kuti anthu ngati Wodemaya alipo kale m’dziko muno ndipo akufunikira kugwilidwa dzanja.

“Uyu mu zone yanga Ali number 1, wodemaya wanu uja number 2, zomwe wapanga nyamata waku Ghana uja, wathuyu wapangapo, koma sitidatengere serious chifukwa ndi mmalawi nzathu. Mkaziyu ntchito amagwira, vuto support.

“Tiyeni timphunzire kuyamikilana amalawi okha okha, mibadwe yansanje ndiimene, ikuthayi, generation yathu ino tidzale chikondi, muchikondi muli dzipaso zambili zomwe zizapindulire dziko komaso Ife yeni.

“Travel with Mervis akuyenekera drone, good camera, good phone, ndi mnyamata special ojambula. Zomwe wapanga nzathu waku Ghana uja, uyuyu amapanga, koma sikuti tikunyoza waku Ghana uja no, tikumuthokoza kwambili, watiphunzitsa,” watelo munthu wina pa fesibuku.

Advertisement