Mpira wa miyendo wa atsikana ukuyenda bwino – Migogo

Advertisement

Mtsogoleri wa  bungwe la National Women’s Football a  Adelaide Migogo wati mphoto imodzi  yomwe Malawi yapeza yomwe wawina Leticia Chinyamula kukhala osewela yemwe adzakhale wapamwamba mtsogolomu zawonetsa kuti osewerawa ali ndi kuthekera kochita bwino kwambiri mtsogolomu akamalowa nawo mu mipikisano yambiri.

Poyankhula  ndi wayilesi ina m’dziko muno a  Migogo apempha boma kuti lithandize mpira wa miyendo wa atsikana kuti adzitha kulowa mu mipikisano yochuluka osati ya COSAFA yokha.

“Tikungopempha ma kampani kuti ayike ndalama zawo mu women’s football chifukwa ndi imene ikuyika Malawi pa Map, tikupempha boma kuti litithandize tilowe mu mipikano yambiri,” Mugogo anafotokoza.

Mtsogoleri wa Football Association of Malawi (FAM) a Fleetwood Haiya ati ndi okondwa chifukwa cha kupeza mphoto imodzi kulekana mkubwera manja-manja ndipo ati awonetsetsa kuti masewero a  mpira wa miyendo wa atsikana apite patsogolo ndipo ati athandizapo mochulukira.

Football Association of Malawi (FAM) president Fleetwood Haiya
Tionetsetsa kuti mpira wa miyendo wa atsikana upite patsogolo – Haiya.

Leticia Chinyamula yemwe ndi osewela wa Ascent academy women’s football kuno kumudzi,  walandila mphotoyi ku Sandton m’dziko la South Africa.

Tabitha Chawinga wakanika kusankhidwa kukhala osewera wa pamwamba wa  mchaka cha 2023, m’malo mwake watenga ndi Recheal Kundananji wa m’dziko la Zambia.

Mu ndemanga zawo anthu pa tsamba la mchezo la COSAFA ati sizinawagwire mtima kuti  mphoto zambiri pa mwambowu zamka m’dziko la South Africa.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.