Malawi ali patsogolo pankhani yoteteza Njovu

Advertisement

Bungwe la Elephant Protection Initiative (EPI) lati dziko la Malawi lachita bwino pa nkhani yoteteza njovu ndipo laposa maiko oposa 24 amchigawo cha Africa omwe ali pansi pa bungweli.

Poyankhulapo pa za nkhaniyi ndi wailesi ina yofalitsa mawu dziko muno, Nkulu wa Parks and Wildlife, a Brighton Kumchedwa ati njira monga kukhazikitsidwa kwa ndondomeko ya National Elephant Action Plan kwathandiza kuthana ndi nchitidwe wopezeka ndi nyanga za Njovu.

Elephant Malawi
Izi ndizonyaditsa- Kumchedwa.

“Izi ndi zonyaditsa kwa ife a Malawi ndipo ndondomeko ya National Elephant Action Plan yomwe idakhazikitsidwa ndicholinga chothana ndi nchitidwewu yathandiza kuti Malawi akhale patsogolo pankhani yoteteza njovu m’dziko muno,” atero a Kumchedwa.

Iwo atsindika kunena kuti Parks and Wildlife ipitilira kuika malamulo oonetsetsa kuti njovu zikutetezedwa dziko muno ndi kuthetsa nchitidwe ochita malonda a nyanga zake.

Bungwe la Elephant Protection Initiative lidakhadzikitsidwa mchaka cha 2014 ndi cholinga chofuna kuteteza njovu za nchigawo cha Africa.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.