Anthu ena okhala mu Mzinda wa Zomba ati zinthu mdziko muno zikuvuta kwambiri pankhani ya achinyamata kupeza ntchito, njala komanso kukwera kwa zinthu chifukwa chipani cha MCP chikufuna chidzilamulira chokha osafunanso kumagwiritsa ntchito mfundo zachipani cha UTM.
Malinga ndi a Patrick Gremu amene amachita malonda mumzindawu omwe Malawi24 yayankhula nawo, ati chipani cha MCP chidalowa m’boma chifukwa chamgwirizano wa Tonse Alliance ndipo pachokha sichikadatha kupambana pachisankho chachibwereza cha chaka cha 2020 ndiye chisamanamize anthu kuti ndichipani cholamula.
A Gremu adapitilira kunena kuti mtsogoleri wadziko lino Lazarus Chakwera akulakwa kwambiri posamamugwiritsa ntchito wachiwiri wake Saulos Chilima chifukwa ndiyemwe adapangisa kuti mgwirizano wa Tonse Alliance upambane pachisankho chachibwereza cha 2020.
Pamenepa iwo adatinso zinthu mdziko muno zikuvuta kwambiri pankhani ya achinyamata kupeza ntchito, njala komanso kukwera kwa zinthu chifukwa chipani cha MCP chikufuna chizilamulira chokha.
“Anthu omwe amuzungulira mtsogoleri wadziko lino Chakwera ndiwomwe akumulakwitsa popeza ndiwomwe akumamuuza maganizo olakwikwa kuti atsamamugwiritse ntchito Chilima.” Adatero a Gremu.
Poyankhulanso ndi Malawi24, mkulu wina ochita malonda kwa Mpondabwino mu Mzinda wa Zomba a Jeremia madzulo adati ngakhale mgwirizano wa Tonse Alliance muli zipani zambiri komabe anthu akudziwa kuti Chilima ndi amene adagwira ntchito yayikulu kuti apambane choncho a MCP asamadzinamize kuti ndi chipani cholamula.
Madzulo adati mfundo zomwe zili mu manifesto achipani cha UTM ndi zomwe zidakopa anthu kuti avotere mgwirizano wa Tonse Alliance ndiye chomwe angadziwe achipani cha MCP ndichoti pawokha sichipani cholamula koma ndi mgwirizano omwe ukulamula dziko lino.
Posachedwapa, Nduna yadza maboma ang’ono a Richard Chimwendo Banda pamodzi ndi akulu akulu achipani cha MCP adachititsa nsonkhano wandale ku Naisi Boma la Zomba ndipo adauza anthu pansokhanowo kuti chipani chawo ndichomwe chikulamula mdziko lino zomwe sizidasangalatse anthu okhala m’bomali.
Follow us on Twitter: