Ntchembere zandonda zagwa

Advertisement
Armyworms

Unduna wa ulimi, ulimi wa nthirira ndi chitukuko chamadzi wati ntchembere zandonda zikuonononga mbewu zosiyanasiya m’madera ambiri m’dziko muno.

Mbozizi zagwa chifukwa chakusintha Kwa nyengo m’madea ambiri mdziko muno. Izi zili chomwechi potsatira mvula yankutho yomwe ikumasatana ndi dzuwa la nnanu ndipo nyengo yotero ndiyomwe imapangisa mbozi za ntunduwu kuchulukana.

“Ntchembere zandonda zimagwira mbewu zomwe zili mugulu za udzu monga chimanga, mapira, mpunga, ndi zina zotero. Ndipo zimaononga kwambiri ngati palibe njila zothanirana nazo,” watero m’mlembi wa ku undunawu a Grey Phiri kudzera mu chikalata chomwe atulusa.

A Phiri alangiza alimi kuti aziyendera mbewu zawo pafupipafupi kut aziona ngati mbewu zawo zagwidwa ndi mbozizi.

Zina mwa zizindikiro ndi monga kubooka kwamasamba a mbewu zawo, kupezeka kwa timbozi tamtundu wa gilini koma tamitu ya kuda.

Alimi akaona zina mwa zizindikilozo, akuyenera kukanena ku ma ofesi azaulimi omwe ali mdera lao ndipo akauzidwa njira zomwe angatsate kuti athane nazo komanso akapasidwa mankhwala oti azikathira mbewu zawozo.

Mchikalatacho, a Phiri auza alimi onse kuti mankhwalawa ndiaulele.

“Alimi akupemphedwa kukanena ku police yomwe ali nayo pafupi ngati akuudzidwa kuti alipire mankhwalawa,” a Phiri atero.

Advertisement