Awaimitsa pa ntchito kwa miyezi iwiri kamba kosavala thayo

Advertisement

Muthokoze kuti mabwana anu alibe nazo ntchito ndipo boma la Malawi sililabadila zotelezi koma enanu bwenzi mutaimitsidwa pa ntchito kamba kosavala thayo.

Ogwila ntchito ena a mmboma mu dziko la Uganda aimitsidwa pa ntchito kwa miyezi iwiri ati kamba sanavale molongosoka popita ku ntchito.

Ku Uganda abambo osavala thayo aimitsidwa panchito.

Malinga ndi tsamba losindikiza nkhani la CGTN lati abambo asanu ndi m’modzi (6) a mu dziko la Uganda auzidwe kuti asaonetse chipumi chawo ku ntchito kwa miyezi iwiri.

Abambowo akuti adapezeka kuti anapita ku ofesi pakhosi palibe chingwe.

Abambowo amene akuti amagwila ntchito mmboma mu dzikolo anauzidwa kuti sanavale molongosoka ndipo pa chifukwa chimenecho akuyenela kaye kukapuma kuti aphunzile mavalidwe abwino.

Ku Uganda anakhazikitsa lamulo lokhudza kavalidwe kwa anthu ogwila ntchito mmboma.

Malinga ndi malamulo awo ati abambo akuyenela kuvala thayo nthawizonse akugwira ntchito.

Mu malamulowo ati amayi saloledwa kuvala chachifupi choonetsa maondo.

Advertisement

90 Comments

  1. kkkkkkkkkkkkk ndikanagona osaseka nanuso alembi mwayitola patiyimeneyi kkkkkkkkkk sanasowa pomuyimisila ali tinamizile tayi koma zinazi kkkkkkkkkk ayise kuyambila lelo uzifhala tayi

  2. Hahahaha… kusunga mwambo. Pali ntchito zina zomwe zimakhudzana kukopa anthu, bizinesi, u loya, zimafunikadi uvala bwino. Chomwe chimadziwitsa kuti munthu ndi wa khalidwe labwino, wa mwambo, okhulupirika, komaso wa ukhondo, ndicho kuvala thayo (chingwe pakhosi). Munthu suyenera ukhala opanda thayo ku ofesi. Ndikusalemekeza ntchito, Ofesi, komaso organization yomwe munthu ukugwira ntchito. Ntchito za mu field monga, uchikumbe, ulangizi, ukazitape (CID) umayenera ukhala munthu wamba. Tchito ya ku mortuary, yobaya anthu ma jakisoni, ku prison, mu restaurant, mu bala, zili ndi mavalidwe akeso. Mini, see through, body pants, ndi zovala ku ma party, kuphwando, ku club, ku ma entertainment center ndi tourism industry. Cholinga ndikuitanila ma kasitomala.

    1. Kkkkkkkkkk. .. Ndipo simukunama. Zokhwefula ndi za anthu obvina ndiso oyitanira ma minibasi, asowa chochita womwe amakhala ndi makolo awo, oyenda yenda popanda cholinga pamsewu.

  3. Nkhaniyi yongopeka ,a Mw24 anasowa nkhani yowauza anthu, nanga imeneyi ndinkhani yoti alembe? Last month anazalemba kuti ma trouser onyenya mmaondo avuta pa Malawi. Hahahahahaha. Ngati kulibe zolembe kapumuleni akuluakulu.

  4. Pali ndi tchito zakedi zofunika necktie nanga builder,plumber,mechnique angavale thayo?Thayo ali demand kutchito zonse zaboma kuphatikiza kuma bank yes valani mathayo olo kutethe.

    1. Hahahaha ma dad goes to work without tie bt he alwayz look smartdescent. U might wear a tie and still look undescent u knw that?? Kuma interview sikuntchito.

    2. Hahahaha ma dad goes to work without tie bt he alwayz look smartdescent. U might wear a tie and still look undescent u knw that?? Kuma interview sikuntchito.

  5. Ndizaku Uganda izi osati Ku Malawi ayi Azibambo ogwila ntchito za Boma okwana 6 ayimitsidwa ntchito chifukwa chovala thayo mwamalamulo awo nawo azimai ogwila ntchito za Boma saloledwa kuva zazifupi zoonetsa maondo nkhaniyo ikutero ndithu

    1. N’THELADI KUSAMVETSESA NDI MATENDA: KUTUKWANA AKU UGANDA PA LAMULO LAO, KUYAMIKILA KU RSA: MWATI MULI NDI LAMULO PA BANJA LANU-INU?

    2. NO apa sipanachulidwe KT Malawi or Japan ,Nigeria tikut zko kungokhala nd malamulo opepera sitkusamala KT kaya nd k UK or Germany tukukamba zamalamulo opepera

Comments are closed.