Muthokoze kuti mabwana anu alibe nazo ntchito ndipo boma la Malawi sililabadila zotelezi koma enanu bwenzi mutaimitsidwa pa ntchito kamba kosavala thayo.
Ogwila ntchito ena a mmboma mu dziko la Uganda aimitsidwa pa ntchito kwa miyezi iwiri ati kamba sanavale molongosoka popita ku ntchito.

Malinga ndi tsamba losindikiza nkhani la CGTN lati abambo asanu ndi m’modzi (6) a mu dziko la Uganda auzidwe kuti asaonetse chipumi chawo ku ntchito kwa miyezi iwiri.
Abambowo akuti adapezeka kuti anapita ku ofesi pakhosi palibe chingwe.
Abambowo amene akuti amagwila ntchito mmboma mu dzikolo anauzidwa kuti sanavale molongosoka ndipo pa chifukwa chimenecho akuyenela kaye kukapuma kuti aphunzile mavalidwe abwino.
Ku Uganda anakhazikitsa lamulo lokhudza kavalidwe kwa anthu ogwila ntchito mmboma.
Malinga ndi malamulo awo ati abambo akuyenela kuvala thayo nthawizonse akugwira ntchito.
Mu malamulowo ati amayi saloledwa kuvala chachifupi choonetsa maondo.
90 thoughts on “Awaimitsa pa ntchito kwa miyezi iwiri kamba kosavala thayo”
Comments are closed.

Kkkkkkkkkkkkkkkkk minyama yachulukila akapungulitse kkkkk
Bwanayo ndiwamitsala
Ndiye mwati thayo?Nkhani yongokambirana kaya.Munthuyo sanali maliseche ayi.
here in jamaica we dont knw thayo anymore……
kkkkkkkkkkkkk ndikanagona osaseka nanuso alembi mwayitola patiyimeneyi kkkkkkkkkk sanasowa pomuyimisila ali tinamizile tayi koma zinazi kkkkkkkkkk ayise kuyambila lelo uzifhala tayi