A Mutharika akukhala ngati amisala – watelo Lucius Banda

Advertisement
lucius banda

Zimene ananena a Mutharika mu boma la Mangochi zoti phungu mmodzi osokonekela akudana ndi mgwilizano umene uli pakati pa UDF ndi DPP zapsetsa mtima phungu wa dera la Kumpoto mu boma la Balaka a Lucius Banda.

 

Peter Mutharika president
A Mutharika ku Mangochi

A Banda amene anena kuti chala cha a Mutharika chimaloza iwo ngakhale a Mutharika sadawatchule dzina atulutsa chikalata chokwiya ndi zimene anayankhula a Mutharika.

Malinga ndi chikalata chimene atulutsa a Banda, iwo ati ndi okhumudwa ndi zimene a Mutharika analankhula pa msonkhano wawo. A Banda ati iwo mukudziwa kwawo, zipani za UDF ndi DPP sizili pa mgwilizano.

“Zimene anayankhula a President, anayankhula motsogozedwa ndi umbuli chabe,” atelo a Banda.

Iwo aonjezelapo kuti a Mutharika akunyengedwa ndi kupusitsidwa ndi anthu owazungulila pa nkhani za ubale wa zipani ziwirizi.

lucius banda
Lucius Banda

“Ine ndikudziwa kuti palibe mgwilizano umene unasayinilidwa ndi zipani za DPP ndi UDF, ndiye akamati pali mgwilizano ndikudabwa,” atero a Banda.

Iwo aonjezelanso ndi kuchenjeza a Mutharika kuti asiye kuthililapo ndemanga pa nkhani zosawakhudza poopa kuti azayaluka.

“Ndikumema a Mutharika kuti asiye kuikapo mlomo pa nkhani zomwe palibe. Iwo akapitilza kulankhula kutele azayaluka ngati osokonezeka, obalalika ndinso wamisala,” atero a Banda.

Advertisement

3 Comments

Comments are closed.