Dedza Dynamos yatola chi 100 million 

Advertisement

Kunali kumwemwetera chakumasanaku ku Dedza pamene timu ya Dedza Dynamos yatembenuza chikwangwani nkukhala Premier Bet Dynamos kutsatira mgwilizano omwe timuyi yasayinira ndi kampani ya Premier Bet wandalama zokwana 100 miliyoni kwacha.

Kampaniyi yati iziperekanso ndalama zokwana K200,000 kwa ochemelera wapamwamba, K100,000 kwa katswiri osewera m’modzi pamwezi, komanso K500,000 kwa osewera mbambande kumathero a season ya 2024.

Mkulu wa timuyi, Hastings Mpanbira, wayamikira kampaniyi komanso wati ndi onyadira kwambiri kaamba kathandizoli ponena kuti liwathandiza kwambiri m’chaka chimenechi.

Trevor Whitaker, yemwe ndi ka kampani ya Premier Bet anati iwo ndiwokhutira malingana ndi momwe timu ya Dedza ikuchitira.

Mkulu wa bungwe la Football Association of Malawi (FAM) a Fleetwood Haiya wathokoza kampaniyi kaamba kopereka thandizoli ku timuyi.

Pakadali pano timuyi ili pa number 13 mu Tnm Super League ndimapoyintsi okwana atatu.

Advertisement

One Comment

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.