Ukadaulo ndi ukatswiri ndi  yankho ku Chitukuko- Chakwera

Advertisement

President Lazarus Chakwera  wati ukadaulo ndi ukatswiri mwa achinyamata ndiofunika kwambiri pa chitukuko cha dziko la Malawi.

Pa chifukwa ichi, Chakwera wati mpofunika kuti maganizidwe akuya  mdziko  muno apatsidwe chilimbikitso chokwanira.

Poyankhula pa mwambo okumbukira tsiku la luso ndi kufukula nzeru zozama, ku Bingu International  Convention Centre (BICC) mu mzinda wa Lilongwe, Chakwera  anatchula ma ina a William Kamkwamba, Ernest Andrew, John Sailesi, mwa ena, ngati zitsanzo za iwo adavumbulutsa nzeru za kuya mdziko muno.

Mtsogoleri wa dziko linoyu anapempha anthu achuma kuti alowetse ndalama zawo ku anthu amene ali ndi nzeru zakuya kuno ku Malawi.

A Chakwera anawonjezera kuti dziko lapansi likukumana ndi mavuto  a nkhaninkhani amene akuopsyeza chitukuko cha dziko la Malawi ndipo ati mpofunika kupeza mayankho mothandizana kudzera mu mzeru zakuya.

“Zija zomangopita m’misonkhano mkumakangodya kapena kumakangopeleka madando kapena kumakangowonelera ngati mpira  ndi zamakedzana, ino ndi nthawi yokonza mayankho athu ncholinga choti tikamakumana ndi mayiko ena tizikawamema kuti atipatse kuthekera kokwanilitsa masomphenya athu chifukwa zoti tichite tikuzidziwa kale” anatero a Chakwera.

M’mau awo Mlembi wamkulu m’boma, mayi Colleen  Zamba,   anati kusintha kwa kachitidwe ka zinthu m’boma kakuthandiza kwambiri maunduna ndi magawo onse a boma.

A Zamba  ati mpofunika kuonetsetsa kuti izi zikuchitika molingana ndi khumbo lofuna kutenga Malawi kukhala ochita bwino pa chuma pofika chaka cha 2030.

Kukhazikitsidwa kwa nthambi yofukula luso ndi nzeru zozama mu ofesi ya mtsogoleri wa dziko ndi kofunika kwambiri ponena kuti kuthandiza kuwunikira magawo  ochuluka, atero mayi Zamba.

Mu chaka cha 2002 bungwe la United Nations linakhazikitsa 21 April kukhala tsiku lokumbukira nzeru zakuya ndi luso (World Creative and Innovation Day).

Tsikuli linakhazikitsidwa pofuna kuwonetsa kufunika kwa luso ndi nzeru zakuya ku dziko lapansi ndipo Malawi ikupitiliza kukondwera tsikuli pansi pa mutu oti “Kupanga ndi kutumphula luso  la Malawi yemwe tufuna”.

Pa mwambowu ma unduna a zokopa alendo ndi unduna wa migodi apambana kukhala ma unduna okhawo omwe atumphula nzeru mwakuya, ndipo alandila thandizo la ndalama zokwana US$40,000  aliwonse kuti apitilize kukwanilitsa malingaliro a luso la unduna wawo.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.