Ku Malawi munthu osasuta fodya kuyenda mtunda osachepera makilomita mazana asanu osapumako fungo la fodya ndichinthu chamtengo wapatali chofanana kuuzidwa ndi Yesu Mkhrisitu mwiniwake kuti machimo ako akhululukidwa ndipo uli mbali imodzi ya ufumu wa Yehova.
Lero zindikilani kuti ngakhale simusuta fodya wamtundu uliwonse, moyo wanu uli pachiopsezo chodwala matenda kamba ka anthu amene amasuta fodya mwachisawawa ndipo munthu osasuta ndiyemwe ali pa chiopsezo kwambiri kuposa osutayo.
Chizolowezi chosuta fodya m’malo opezeka anthu ambiri monga m’misika, m’mabwalo azamasewero komaso m’misewu chikukulirakulirabe kufikira poti mwana wa zaka zisanu yemwe makolo ake samudziwa fodya akumatha kusiyanitsa fungo la fodya wamba ndi fungo la chamba kaamba ka anthu osuta fodya mwachisawawa.
Choncho, zadziwika kuti palibe yemwe angakane kuti kusuta mwachisawawa pang’ono ndi pang’ono anthu kukuwalowa m’magazi ndipo akuvomereza mosazindikira zotsatira za mchitidwewu monga akunenera Jourbert Jere yemwe wati anatsala pang’ono kukomoka ndifungo lafodya.
“Kwa nthawi zingapo ndakhalapo okhudzidwa ndi mchitidwe osuta paliposewu makamaka ku misika ndi kubwalo lazamasewero la Kamuzu komwe ndimapita kukaonera mpira wa miyendo. Izi zandichitikira kangapo ndipo ndikapuma fungo lafodya ndimavutika mapumidwe ndipo ndimayamba kudwala chimfine ndi chifuwa,” anatero a Jere.
Pothirirapo ndemanga, mkulu wa Drug Fight Malawi a Nelson Zakeyu anati fodya aliyense ali ndi poyizoni ndipo panthawi yosuta poyizoniyu amafikira anthu amene azungulira munthu wosutayo zomwe zikutanthauza kuti anthu ambiri amasuta fodya kaamba kakhalidweli koma samadziwa.
“Zoona zake ndizakuti osuta komaso osasuta yemwe amapuma mpweya wa fodya, onse ali pachiopsezo chodwala matenda odza kaamba kafodya koma opuma mpweya wafodyayo ndiyemwe ali pachiopsezo kwambiri chifukwa ndiyemwe amakoka mpweya wambiri kuposa osutayo,” anatero a Zakeyu.
Koma ndichifukwa chiyani anthu amasuta fodya malo aliwonse kuphatikiza m’misewu, m’matawuni, mmisika ndimalo ena ndi ena?
Mathews Banda yemwe anali ndi ndudu m’manja mwake nthawi yomwe amafusidwa izi kumsika wa Blantyre anati: “Ndimasuta malo aliwonse chifukwa ndimomweso timapangira ndimadzi akumwa. Aliyese amamwa madzi posatengera malo omwe ali. Nkhani imakhala yothetsa ludzu. Choncho ndichifukwa chake mumaona anthu akusuta paliponse.”
Komabe ngakhale zili choncho, mkulu odziwika bwino pa nkhani za ufulu wa anthu a Billy Mayaya ati kusuta m’malo ngati akunenedwawa ndichinthu choopsa kumbali ya umoyo wa anthu komaso kumbali ya ufulu wa anthu osasuta.
A Mayaya anati ndikulakwa kusuta fodya wamtundu uliwose malo omwe pali anthu osasuta komaso pomwe pali ana ndipo ati anthu osutawa akuyenera kukhala ndi malire a malo osutira fodya.
Pophera mphongo zomwe anena a Mayaya, mtsogoleri wa Malawi Congress of Trade Union (MCTU) a Luther Mambala anati chitha kukhala chinthu chabwino ngati boma litaletsa kusuta fodya m’malo omwe mumapezeka anthu.
Iwo anati boma likuyenera kuika zilango pa munthu aliyese opezeka akusuta fodya mmalo omwe akunenedwawa pofuna kupulumutsa anthu osasuta omwe akuzuzika pazoipa zomwe sanazipange.
Nanga anthu achipembedzo akuti bwanji ndi nkhaniyi? M’modzi mwa azibusa odziwika bwino mdziko muno, a Daniel Walusa, ati khalidweli likuzuzaso akhilisitu ochuluka omwe mosadziwa kanthu amapuma mpweya wa fodya.
“Kusuta ndikoipa. Bukhu lopatulika limatifusa Ku Yesaya 55 ndime ya 2 ikuti; ‘Bwanji inu mulikutayila ndalama chinthu chosadya ndikutayira malipiro anu zosakhutitsa? Mverani ine mosamalitsa, nimudye chimene chili chabwino, moyo wanu nukondwere ndizonona’.”
Abusa a Walusa anati anthu osasuta asamakakamizidwe kusuta mwamtundu ngati uwu ndipo anaonjeza kuti fungo la fodya ndinyasi pamunthu okhulupilira Yehova ndiye boma liletse kusuta fodya paliponse.
Koma nanga boma likudziwa kuti anthu amasuta fodya pali ponse? Nanga likudziwa kuti mchitidwewu ndikuphwanya ufulu wa anthu osasuta? Kodi nanga bomalo litani pofuna kuthandiza nkhawa za anthu ambiri omwe alipempha kuti liletse kusuta paliponse?
Adrian Chikumbe ndi mneneri wa boma mu unduna wa za umoyo ndipo wati boma likudziwa ndithu kuipa kwa kusuta paliponse.
“Mogwirizana ndi ufulu wa anthu, aliyense ali ndi ufulu wokhala pomwe pali chilengedwe chabwino choncho boma lipanga lamulo loletsa kusuta malo omwe pali anthu. Komabe izi zikudalira mgwirizano wa mbali zingapo podziwa kuti ntchitoyi siyophweka,” watero Chikumbe poimilira boma.
Iye wati azitsogoleri m’maboma atha kupanga chilichose pofuna kuthetsa mchitidwewu mogwilizana ndi lamulo la za chilengedwe la ‘Environmental Protection Act’ kufikila boma litakhazikitsa lamulo loletsa mchitidwewu.
Ndichifukwa chiyani kuli koyenera kuletsa kusuta m’malo omwe muli anthu?
“Kupuma mpweya wafodya yemwe wina akusuta ndikoopsa ku umoyo wamunthu kaamba koti anthu ozungulira munthu osutayu amapuma mpweya wafodyawo ndipo pali umboni woti mchitidwewu umayambitsa matenda,” malamulo otetezera anthu ku fodya pa dziko lapansi amatero.
Kuletsa kusuta palipose sikuteteza opuma mpweya wa fodya okha komaso ngakhale osutawo atetezeka kamba koti izi zichepetsa poyizoni yemwe amalowa mmatupi mwaosutawo komaso omwe amapuma mpweya oonongekawo.
it will be a great deal……….