Mwanadala si wamphamvu kuposa mkulu wake – yatero Castel

Advertisement
malawi-gin

Kampani yofulura bibida ya Castel yasutsa mphekesera zomwe zikumveka ndi anthu ena okonda chokumwa cha ukali kuti mowa wa gin wang’ono okhala mubotolo la 330ml ndiwamphamvu kuposa okhala mu botolo lalikulu la 750ml.

Hammerson Kanyelere wa ku Lilongwe yemwe amakonda mowa waukaliwu wati gin wang’ono ndiwamphamvu kuposa wamkulu.

“Olo m’mene amawawira baby gin amaposanso gin wamkulu zomwe zimasonyeza kuti baby gin ndi wa mphamvu,” anatero Kanyelere.

Kafukufuku yemwe tinapanga malo ambiri omwera mowa (Liquor Shop) mu mzinda wa Lilongwe anayima pa mfundo yokuti gin wang’ono ndi wamphamvu kuposa wamkulu.

Poyikirapo ndemanga mkulu owona za malonda ku Castel komwe mowawu umapangidwa a Lavern Chitakata alesa mphekesera zonsezo ponena kuti mowa onsewo ndi chimodzimodzi.

“Vuto ndilokuti anthu gin wang’ono amamuphweketsa choncho amamaliza mu nthawi yochepa zomwe zimapangitsa kuti aledzere naye mwachangu,” iwo anatero.

Anapitilira kufotokoza kuti “Gin wamkulu ndi wang’ono onse ndi 43% palibe kusiyana ndipo tinapanga baby gin kuti anthu amene ali ochepekedwa azitha kumufikira pozindikira kuti anthu ena amamwa mowa wina wamphamvu osadziwika bwino owononga matupi awo pomwe baby gin ndi ovomerezeka ndi bungwe la Malawi Bureau of Standards.”

Mu zaka zambuyo kunalinso Malawi gin wina okhala mu sacheti komanso wina okhala mubotolo laling’ono la 200ml koma anthu sanandawuleko nkhani ngati izi. 

Advertisement