Wamwalira pampikisano wazidakwa atagugudiza matoti 42 a kachasu

Advertisement
Malawi24.com

Bambo wina wazaka 49 wa m’mudzi mwa Binya kwa mfumu yaikulu Kwataine ku Ntcheu, watsikira kulichete atamwa matoti 42 akachasu pampikisano wazidakwa opapira bibida omwe unachitika dzulo mbomali.

Nkhani yonse ikuti dzulo lolemba pa 11 March m’mudzi mwa a Binya m’bomalo munachitika mpikisano okuntha bibida ndipo malemuwa omwe dzina lawo ndi a Biliat Moffat analowa nawo mumpikisanowu.

Apa a Moffat anaonetsa luso lawo lokumwa chakumwa cha ukalichi, ndipo atangotsiliza kumwa matoti 42 akachasu a Moffat anagwa pansi.

Apa anthu ena anathamangira kuchipatala ndi mkuluyu komwe achipatala anapeza kuti mkuluyu wafa kamba kakumwa bibida osadyera.

Pakadali pano mneneri wa apolisi m’bomali a Jacob Khembo atsimikiza za nkhaniyi.

Advertisement