Sitinagulitse nsika wa Kamba – yatsutsa khonsolo ya nzinda wa Blantyre

Advertisement
Blantyre City Council

Khonsolo ya nzinda wa Blantyre yatsutsa  mphekesera zomwe zikumveka kuti yagulitsa nsika wa Kamba kwa mponda matiki wina wa chimwenye.

Sabata yomwe ikungothayi kwakhala kukumveka manong’onong’o kuti khonsolo ya nzinda wa Blantyre yagulitsa nsika wa Kamba kwa munthu wina yemwe akuti akufuna kupangapo chitukuko china.

Tsamba lino linavetsedwa kuti ochita malonda munsikawu anagwirizana kuti apite ku bwalo la milandu kukatenga chiletso choletsa khosoloyi paganizo lake pofuna kugulitsa nsikawu.

Koma nkulu wa khonsoloyi Dennis Chinseu, walangiza anthu m’dziko muno kuti asakhulupilire mphekesera zomwe zikuvekazi ponena kuti ndi bodza la nkunkhuniza.

Poyankhula ndi nyumba zina zosindikiza nkhani m’dziko muno, a Chinseu afotokoza kuti pali khumutcha wina ochokera munzinda wa Lilongwe yemwe waonetsa chidwi chofuna kutukula nsikawu.

Iwo ati munthuyu akufuna kuchita mgwirizano ndi khonsoloyi kuti pamalowa pamangidwe nsika wa tsopano komanso wa makono (shopping mall) ndipo akuti ntchito yomangaso nsikawu igwiritsa ntchito ndalama zoposera 3 biliyoni Kwacha.

A Chinseu ati izi zichitika pansi pa masomphenya a khonsoloyi ofuna kukozanso misika yonse ing’onoing’ono yomwe idalowa pansi kapena yomwe idasiiratu kugwira ntchito munzindawu, ndipo Kamba ndi umodzi mwa iyo.

Advertisement