Anthu akhungu la chi alubino ati miyoyo yawo ili pachiwopsezo pomwe chisankho chikuyandikira

Advertisement
Albinism

Anthu a wulumali wa khungu la chi alubino ati miyoyo yawo ili pachiwopsezo ndipo ali ndi mantha pomwe chisankho chosankha mtsogoleri wadziko, aphungu akunyumba yamalamulo komanso makhansala chatsala pang’ono kuti chichitike m’dziko muno.

Wapampando wa bungwe la anthu akhungu lachi alubino m’boma la Zomba a William Masapi ndi omwe ayankhula izi ndi Malawi24.

A Masapi apempha mafumu komanso adindo kuti ateteze miyoyo ya anthu akhungu lachi alubino kwina kulikonse komwe akukhala.

Iwo ati kafukufuku akusonyeza kuti anthu akhungu la chi alubino amaphedwa kwambiri m’dziko muno mukamachitika zisankho chifukwa chazikhulupiliro.

Pamenepa, iwo ati munthu wakhungu la chi alubino adalengedwa ndi Mulungu ndipo ali ngati munthu wina aliyense choncho palibe chifukwa chokuti anthu adziwapha pofuna zizimba kapena kulemera.

“Tipemphe mafumu m’dziko muno komanso adindo kuti ateteze anthu akhungu lachi alubino pomwe m’dziko muno mwatsala pang’ono kuti muchitike chisankho chapatatu chifukwa nthawiyi miyoyo yathu imakhala pachiwopsezo,” adayankhula motero a Masapi.

M’dziko muno mukuyembekezeka kuchitika chisankhochi mwezi wa September chaka cha 2025.

Advertisement