Timu ya FCB Nyasa Big Bullets yadzudzula ena mwa otsatira team’yi pankhani yokhudza ziwawa zomwe zidachitika pa bwalo la masewero la Kamuzu itagonja ndi timu ya Silver Strikers ndi chigoli chimodzi kwa chilowere.
Izi ndimalingana ndi chikalata chomwe akuluakulu a timuyi atulutsa ponena kuti iwo akugwilizana ndi zomwe bungwe la Super League of Malawi (SULOM) lakhazikitsa kuti lizindikire omwe adachita za upanduzi.
Timuyi yati ili ndichisoni komanso ndiyokhudzidwa kamba kakuonongeka kwa bus ya Silver yomwe idaswedwa potsatira ziwawazi.
Kalatayi yati Bullets imakhulupilira kuti masewero amabweretsa msangulutso pakati pa anthu osiyasiyana kotero timuyi yati chitetezo ndichofunika kwambiri pamasewero ampira.
Tiimuyi kudzera mchikalatachi yatinso ndiyodzipereka kuthandiza kukonzetsa basiyo.
Pakadali pano timuyi ili pa nambala 5 ndi mapointi okwana 14 itasewera masewero asanu ndi anayi.