Azipita Chamkakala – a mabungwe

Advertisement
Masauko Chamkakala

Atha kuona ma demo angati a Jane Ansah naye Masautso Chamkakala chifukwa a mabungwe ndiye akwiya naye. Ati sakuona phindu lake. 

Mabungwe omwe si aboma ati a Chamkala omwe ndi mkulu wa ofesi ya yoyang’anira zozenga milandu m’dziko muno, Director of Prosecutions (DPP), akuyenera kutula pansi udindo polephera kugwira ntchito yake moyenera. 

Izi zanenedwa pa msonkhano wa a tolankhani omwe mabungwe a Youth and Society (YAS), National Alliance Against Corruption (NAAC) ndi ena  anakonza mu mzinda wa Lilongwe. 

Poyankhura pa msonkhanowu, mkulu wa Bungwe la  YAS, Charles Kajoloweka wati awona kuti  DPP yakhala ikuthetsa  milandu yomwe inali ku malo ozengera milandu ku court isanafike pamapeto. 

Tikufuna ACB ibwere poyera pasanakwane masiku khumi ndi anayi.

Iwo anapereka zitsanzo za milandu yomwe ina mwa iyo ndi nkhani yomwe yathesedwa posachedwapa yokhunza wachiwiri wa mtsogoleri wa dziko lino a Saulos Chilima  komanso ndi milandu ngati ya pulesidenti wakale a Bakili Muluzi, Cassim Chilumpha, Paramount Holdings ndi ina. 

Kajoloweka anati milandu yonseyi palibe chomwe ofesi ya DPP inabweretsa poyera potengera kuti ikuyenera kutero mogwirizana ndi malamulo a dziko lino . 

“Tikuona kuti malamulo omwe alipo akupelewera , chifukwa chimodzi chomwe chimayenera kuchitika ndi chakuti ofesi ya DPP ikuyenera kupereka zifukwa ku komitii ya nyumba ya malamulo  nthawi yoti ofesi ya DPP yi yathetsa mlandu. Izizi zikusonyeza kuti ngati dziko tikukanika kuthana ndi katangale”, adatero Kajoloweka. 

Iwo anawonjezera ponena kuti nkhani zonse zomwe zikuthesedwa zambiri mwa izo ndi za anthu andale, anthu omwe ali ndi maina komanso omwe ali ndi ndalama koma  amalawi omwe  ndi amphawi sakupeza mwayi umenewo. 

Kajoloweka ati zonsezi zikuchitika chifukwa chosowa  chilungamo popeza omwe ali ndi chuma  ndi omwe akuoneka kuti nkhani zakatangale akuthanazo komano osauka akupezedwa olakwa zomwe  sizikuyenera kutero . 

Iwo ati pazifukwa zonsezi aona kuti mkulu wa ofesi ya DPP atule pansi udindo wake chifukwa akulephera kugwira ntchito yake moyenera. 

Mabungwewa atinso  akufuna Bungwe lothana ndi katangale la Anti-Corruption Bureau (ACB) libwere poyera pasanakwane masiku khumi ndi anayi (14) ndikufotokozera ku mtundu wa Malawi pa ndalama zomwe linagwiritsa ntchito pa milandu yomwe yathesedwayi ndipo akapanda kutero apeza njira zina zoti bungweli liwulure.

Advertisement