Mnyamata wa Form 2 ku Likangala Secondary School akufuna thandizo

Advertisement

Humphry Likaka, mnyamata yemwe akuphunzira ku Likangala Secondary School ku Zomba ndipo ali mu Form 2, ali pa chiopsezo chosiya sukulu chifukwa chosowa thandizo.

Humphry yemwe ndi ovutikitsitsa amakhala ndi malume ake kwa Kazembe omwe ndiwovutika ndipo amachitita kupemphetsa (masikini) mu mzinda wa Zomba kuti apeze chokudya.

Iye wauza Malawi24 kuti moyo wafika povuta popeza akusowa ndalama zolipilira sukulu, chokudya ndi zovala moti nthawi zambiri amapita kusukulu asadadye kanthu ndipo akabwelera kunyumba amakapedzanso kuti kulibe chokudya.

Humphry yemwe adakhala nambala yachinayi (4) pamayeso ake ndipo school ya Likangala Secondary mogwirizana ndi komiti ya PTA idamupatsa satifiketi yomuzindikira kuti ndi m’modzi mwa ana amene akuchita bwino omwe ali form 2, wati khumbo lake ndilokuti adzafike ku yunivesite koma vuto laza chuma ndilomwe lingamulepheretse masomphenya ake.

Iye wapempha anthu akufuna kwabwino kuti amuthandidze ndi ndalama zolipilira sukulu, chokudya, zovala komanso makope ndi zolembera kuti athe kumapita kusukulu mosavutika ndipo wati alinso ndi vuto losawona patali ndipo adati pakufunika magalasi okuti adzivala chifukwa omwe akuvala pakali pano omwenso adamugulira ndi anthu okufuna kwabwino atsala pang’ono kutha.

“Vuto lawumphawi lomwe ndikukumana nalo ndilomwe lingapangitse kuti tsogolo langa lamaphunziro lithere panjira koma ngati pangapedzeke ondithandidza ndikulonjedza kuti maphunziro anga ndifika nawo patali,” adayankhula motero Humphrey.

Omwe akufuna kupereka thandidzo kapena kukumana naye akhoza kuyimbira foni pa nambala iyi 0995 027 920.

Advertisement