Ndime yachiwiri yakalembera wachisankho chapatatu chomwe chidzachitike mwezi wa Sepitembala chaka cha mawa, yayamba bwino m’boma la Zomba ndipo malo onse olembetsera akumatsekulidwa 8 koloko mamawa mpaka 4 koloko madzulo.
Malawi24 idayendera malo olembembetsera monga Matiya Pulayimale, Mponda Pulayimale Sukulu, Dwale, Zomba Stadium komanso Gymkhana Club ndipo idapeza anthu ogwira ntchito abungwe lowona zachisankho, achitetezo komanso mamonita azipani zandale akugwira ntchito.
Mwa malo ena omwe Malawi24 yayendera monga Matiya Pulayimale, Mponda Pulayimale ndi Dwale yapeza kuti zipangizo zolembetsera ziphanso za unzika zidali zisadafike zomwe zapangitsa kuti anthu omwe alibe chiphatso cha unzika asalembetse kalembelayo.
Koma akulu akulu omwe akuyang’anira kalembelayo atiuza kuti zipangizo za Bungwe la NRB zifika nthawi ina iliyonse mmalo olembetserawo.
Ndime yachiwiri yakalembera wachisankho akhala akuchitika Boma la Zomba kuyambira Loweruka pa 9 mpaka pa 22 November ndipo ntchitoyi igwiridwa kwa masabata awiri.