Boma alipempha kuyikapo chidwi potukula masewero oyendetsa galimoto

Advertisement

Gulu la achinyamata omwe amachita masewero oyendetsa galimoto mochititsa kaso a motorsport-spinning pachizungu mumzinda wa Blantyre apempha boma kuti liyesetse kuyikapo chidwi pofuna kutukula masewerowa m’dziko muno ponena kuti ndiofunika kwambiri.

Izi zanenedwa dzulo ku Chilobwe mu mzindawu komwe gululi lomwe likutchedwa Spinners Nest Motorsport linali ndi chilawitso chamasewerowa.

M’mawu ake Geoffrey Jarid yemwe ndiwapampando wagululi anati iwo akukumana ndi mavuto ambiri maka kusowa malo apadera omwe atha kumachitilapo masewerowa.

“Kunena zoona tikukumana ndi mavuto ochuluka chiyambireni masewerowa m’dziko muno. Vuto lalikulu ndikusowekera malo okhazikika abwino omwe titha kumapangirapo  masewero athuwa. Mutha kuona kuti panopa masewerowa tikumapangira m’msewu zomwe ndizosayenera. Ndiye timapempha boma kuti lithandize maka kunkhani yamalo omwe titha kumachitirako masewerowa,” anatero Jarid.

Poyankhapo ngati anakumanapo ndi unduna wazamasewero pamavuto omwe amakumananawowa, Jarid anati akumanapo ndi anthu oyenera osiyanasiyana kuti awathandize ndipo pano akungodikira zotsatila.

M’modzi mwa ochitanawo masewerowa  Blessings Malemba anati iye ndiokondwa kuti masewerowa omwe amangochitika m’mayiko akunja kwa dziko lino tsopano afika.

“Ndine okondwa kwambiri kuti tsopano motorsport yafika ku Malawi ndipo ndili ndichikhulupiliro kuti izi zithandiza dziko lino kukwera pachuma. Mavuto ndiomwe anenedwa kalewo ndipo tikukhulupilira kuti boma lichitapo kanthu,” anatero Malemba.

Masewero a motorsport-spinning amachitika m’mayiko ambiri mu Africa muno monga Zimbabwe, Zambia, South Africa, Nigeria kungotchulapo ochepa chabe.

Advertisement