Boma lapereka nyumba 20 kwa apolisi m’dziko muno

Advertisement
Ken Zikhale Ng'oma handing over the houses

Apolisi ku Ndirande tsopano akhala akusimba lokoma pamene nduna ya zachitetezo a Kenneth Zikhale Ng’oma lero yatsekulira nyumba zamakono zokwana 20 zomwe boma la a  Lazarus Chakwera lamanga mgawo la nyumba 10,000 zomwe zikhale zikumangidwa m’dziko lino.

Kutsatira lonjezo lomwe adachita a Chakwera mchaka cha 2020, pofika lero bomali lamangapo nyumba zokwana 1028, ndipo 20 zi zili mgawo limeneri.

Poyankhulapo pamwambo omwe unaliko lelowu, a Zikhale ayamikira makontalakitala pomanga nyumba zapamwambazi ndipo kotero iwo ati awonetsetsa kuti nyumba zankhaninkhani za achitetezo kuphatikizapo za apolisi zamangidwa ndipo akukhala m’nyumba zolozeka.

A nduna za malo a Deus Gumba anayankhulaponso pa mwambowu ndipo ati boma likufunitsitsa kuti achitetezo azikhala nyumba zabwino ndi cholinga choti azitha kugwira ntchito zawo bwino.

Pofika lero boma la a Chakwera lamangapo nyumbazi m’madera monga Mzuzu, Blantyre, komanso ku Mzimba.

Advertisement