…sukulu yati omwe sapanga nawo gala apelekebe ndalamayi
Pomwe amaona ngati athana nazo zopeleka vindalama vitalivitali, ophunzira omwe amaliza maphunziro pa sukulu ya ukachenjede ya Malawi Assemblies of God University (MAGU), akuyeneraso kupisaso m’matumba ndikupeleka ndalama ya gala yomwe yafika mpaka K250,000.
Sukulu ya ukachenjede ya MAGU yalengeza kuti mwambo otsazikana ndi ophunzira omwe amaliza maphunziro pa sukuluyi uchitika la chisanu pa 24 November, chaka chino ndipo ukachitikira ku Bingu International Convention Center (BICC) munzinda wa Lilongwe.
Koma chatsitsa dzaye kuti njovu ithyoke nyanga ndi mitengo yomwe sukulu ya MAGU yatulutsa posachedwapa kudzera mchikalata chomwe chasainidwa ndi mkulu wa sukuluyi a Albert Newa.
Sukuluyi yati aliyese yemwe wamaliza maphunziro ake a satifiketi ndipo alibe Bachelor’s digili, akuyenera kupeleka K70,000 ya galajuweshoni pamene ophunzira a satifiketi amene ali ndi Bachelor’s digili awuzidwa kupeleka K140,000.
Ophunzira omwe amaliza maphunziro pa MAGU ndipo ali ndi Master’s digili, alamulidwa kupeleka ndalama ya galajuweshoni yokwana K190,000 pomwe omwe amaliza maphunziro a dipuloma akuyembekezeka kupeleka K100,000 yakumwambowu.
Kupatula apo, omwe amaliza maphunziro pa mlingo wa Bachelors, akuyenera kupeleka K140,000 pamene amene amaliza Masters, apeleka ndalama yokwana K190,000 ndipo omwe amaliza maphunziro pa mlingo wa PhD, akuyenera kupeleka K250,000 ya galajuweshoni.
Chomwe chadzetsa tsemwe kwambiri nchakuti ophunzira onse omwe angapange chisankho chosakapezeka ku mwambowu, awuzidwa kuti akuyenerabe kupeleka ndalamayi.
Kuwonjezera apo, sukulu ya MAGU yati ophunzira aliyese amene angawononge kapena kutaya chovala cha galajuweshoni chija chimatchedwa gawuni chija, akuyenera kudzapeleka ndalama yokwana K150,000.
Pakadali pano, anthu m’masamba anchezo adzudzura akuluakulu a sukulu ya MAGU pa mitengoyi yomwe ambiri a kuti ndi chiphinjo kwa ophunzira ochuluka makamaka amene amachokera m’mabanja ovutika.
“Graduation yomweyi mpakana chonchi? When we thought we were done with their exorbitant fees then boom (pomwe timaganiza kuti tathana nazo zopereka fizi) zikubwera izizi…..that’s very unfair to us (sizabwino)……ndalama tilibe anthufe,” watelo munthu wina pa fesibuku.
Mbali inayi anthu ena ati pakufunika kuti owongolera maphunziro awukachenjede m’dziko muno ayambe kuteteza ophunzira kuchiphinjo cholamulidwa kupeleka ndalama za nkhani nkhani zomwe a kuti zina zimakhala zosafunikira kwenikweni.