Akubwela katemera wa Covid-19: boma lati a Malawi 3.8 miliyoni alandila katemera

Advertisement

Mwayi oti moyo utha kubwelelanso mwakale mu chaka cha 2021 ukuoneka waukulu pamene boma lanena kuti katemera othana ndi mliri wa corona afikanso kuno kwathu.

Malingana ndi malipoti a nyuzipepala, boma la Malawi mogwilizana ndi mabungwe ena ali pakalikiliki ofuna kuti dziko la Malawi lipindule nawo pa katemera amene wayamba kupezeka pofuna kuthana ndi kafalidwe ka kachirombo ka corona.

Malipotiwa ati mlembi wamkulu mu unduna wa za umoyo a Charles Mwansambo atsimikiza kuti boma la Malawi likukambilana ndi mabungwe ena monga World Bank ndi IMF kuti athandizepo kuti nafe tithe kupeza mwayi okhala ndi katemela ameneyu.

A Mwansambo aululanso kuti pachiyambi pa zonse, katemelayu sakhala opita kwa anthu onse.

“A Malawi owelengeka ndi amene akhale ndi mwayi olandila katemelayu,” atelo a Mwansambo.

Padakali pano akuti a Malawi 3.8 miliyoni ndiwo angafikilidwe ndi katemelayu. Izi zikusonyeza kuti pa a Malawi 100 alionse, 20 okha ndiwo akhale ndi mwayi olandila katemelayu.

Mu maiko amene ayamba kupeleka katemelayu, anthu ogwila ntchito zachipatala komanso achikulile ndi amene akumakhala ndi mwayi olandila katemelayu.

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

Advertisement