Mumayesa UTM inatha? Kwabwela Fredokiss

Advertisement

Nkutheka UTM ija n’kumadzulo. Kupambwadzidwa pa zisankho zachibweleza zonse anthu mpaka kufika ponyodola kuti palibe chipani koma Chilima basi, chipani cha UTM chayamba kuphukila.

Oyimba nyimbo za a chinyamata amenenso ndi mwana wa nduna yakale yoona za malo a Kamlepo Kalua, Penjani Kalua amene omukonda amangoti Fredokiss walengeza kuti akujoina chipani cha UTM.

Fredokiss amene anapikisana ngati oyima payekha ndipo anagonja ku dera la kummwera la Blantyre, wanena kuti waona kuti tsogolo lake mu ndale lili mu chipani cha UTM chimene chimapeleka mpata kwa achinyamata.

Pa 31 December pano, limene ndi lero, chipani cha UTM chikhala chikulandila Fredokiss ku Zingwangwa kumenenso kukhale phwando la zoimbaimba losangalatsa achinyamata.

Pa chisankho cha chibweleza mu chaka tikutsanzikana nacho ichi, Fredokiss ananjatwa ati kamba amahonga anthu kuti avotele DPP powapatsa ndalama kwawo ku Rumphi. Mlandu wake sunapitilile ati kamba unalibe umboni.

Itatha nkhaniyi analowa mu studio Fredokiss mmene anakayimba nyimbo yodzudzula anthu amene anamukonzekela upandu.

 

 

 

 

 

 

 

Advertisement