A Bullets sangabwele kuti atiwonongele mbiri – Mponda

Advertisement
Mponda

Timu ya mizilazembe yomwe ikutsogolera 2024 TNM Super League m’dziko muno ya Silver Strikers kudzera kwa m’phunzitsi wake Peter Mponda yati timu ya Bullets singabwere pa khomo pawo kuti idzawononge mbiri yawo ya kusagonja chiyambileni ligi.

Pambuyo pa masewelo amene aseweledwe loweluka pa bwalo la Silver pakati pa FCB Nyasa Big Bullets ndi Silver Strikers ku area 47 mu mzinda wa Lilongwe, ndipo ndi masewelo akulu sabata ino Mponda wati akukhulupilira anyamata ake kuti akasewela momwe anasewelera ndi MAFCO pamene anayiswa 6-1 sabata yomwe ino lachitatu.

Mponda wati ligi isongola akatenga ma point atatu a mawa ndipo wati pokasewela ndi Bullets akaonetsetsa kuti akapeze mipata yoyenera yogonjetsela Bullets monga m’mene anachitira ndi MAFCO popeza amamva bwino akamasewera pakhomo, pa bwalo la Silver.

Kalisto Pasuwa mphunzitsi wa FCB Nyasa Big Bullets poyankhula ndi atolankhani a timuyi wati masewelo a mawa ndi ofunika kwambiri ndipo ncholinga chawo kukapambana koma ndi okonzeka kulandira zotsatira zilizonse zomwe zingadze pakutha pa masewelo potengela m’mene Silver ilili.

Silver yomwe pano ili ndi ma points 57 m’masewelo 25 ikusiyana ndi Mighty Mukuru Wanderers ndi ma points 4, pamene ndi Bullets akulekana ma points 13.

Oyimbira Easter Zimba ndi amene atenge ulamuliro wa nkhondo yamawa, pamene Mponda anadandaula za oyimbira Mwayi Msungama lachitatu, ponena kuti oyimbira mpira akuoneka kuti akufuna kuti awaphumitse ligi.

Masewelo a lowelukali anthu akuyenera kupisa mthumba kamba koti mitengo yake yolowera pakhomo ayikusira patsogolo pamene ku open stand mtengo uli K7,000 ndi K15, 000 ku VIP.

Advertisement