Bambo anjatidwa kamba kogwililira ana awiri pa tchalitchi

Advertisement
Mangochi Police

Apolisi ku Makokola m’boma la Mangochi amanga bambo wa zaka 35 zakubadwa, James Phiri pomuganizira kuti anagonana ndi ana awiri omwe ndi pachibale azaka 12 komanso 10. 

Malingana ndi mneneri wa polisi ya Mangochi, Amina Tepani Daudi, anawa amagulitsa samosa pa msika wa pa Makawa pomwe Phiri, yemwe amakonda kugulagula samosa’yu, adagula samosa muwiri ndikuwapatsa ndalama zokwana K1000 ponena kuti akufuna chenje.

Phiri adawatengera anawa kutchalitchi china chomwe sichidamalizidwe, komwe adawagona, ndikuwapatsa K500 n’kuwopseza kuti asakaulule za nkhaniyi.

Malingana ndi Daudi, m’maŵa wake, mayi wa anawa anaona kuti anawa akuvutika kuyenda ndipo amamva ululu ku malo obisika zomwe zinschititsa kuti awapanikize ndi mafunso ndipo anawa adawulula zomwe zidachitika.

“Apa, mayiyu anapita ku polisi kukasuma za nkhaniyi, ndipo apolisi anatengera anawa ku chipatala komwe zotsatira zidatsimikiza kuti adagwiriridwa,” watero Daudi.

Phiri akuyimbidwa milandu iwiri yogonana ndi ana achichepele zomwe ndizosephana ndi gawo 138 la malamulo adziko lino ndipo akaonekera kubwalo lamilandu posachedwa.

Advertisement